Oweluza mlandu Chief Resident Magistrate Rodrick Michongwe wati a Patricia Kaliati akuwaganizira mulandu opanga upo ofuna kupha mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera.
Malingana ndi oweruza mulanduwu, a A Kaliati adachita upo ndi anthu ena awiri omwe mpakana pano a Polisi sanawapeze.
A Michongwe anati anthu omwe akuwaganizira kuti anapalamura mulanduwu ndi a Frank Chinedu ndi Joseph Odala omwe anathawa
Iwo anapitiliza kunena kuti, anthuwa anapalamura mulanduwu pakati pa miyezi ya March ndi June chaka Chino.
Polakhula po omwe akuyimira Boma pa mulanduwu anapempha bwalo la milandu kuti liwapatse masiku asanu ndi awiri, 7, kuti amalize kafukufuku wawo.
Iwowa anati akufuna kuti a Kaliati apitilire kukhala m’manja mwa apolisi mpakana atamaliza kafukufuku wawo.
Koma poyakhapo, a Khwima mchizi, omwe ndi m’modzi mwa omwe akuyimira mayi Patricia Kaliati, anati zomwe a Boma akunena kuti oganiziridwawa asawatulutse pa belo ndi zodabwitsa chifukwa apolisi amayenera kumanga a kaliati atamaliza kafukufuku wawo.
Iwo anatiso mabwalo aperekako kale zigamulo m’mbuyomu kuphatikizapo la supreme kuti kumangidwa kwa munthu kudzitsatira kafukufuku okwanira wamulandu.
A Mchizi anatiso Boma silikuyenera kusungabe aKaliati chifukwa munthu amayenera kumangidwa a Polisi atamaliza kuchita kafukufuku ndipo mabwalo a Milandu anatsindikaso pa zimenezi.
Malinga ndi a Mchizi, Boma likufuna kuwasungabe a Kaliati chifukwa likufuna lidziwafunsa mafunso pomwe anuwake anena Kuti sakufuna kuyakhulapo pa nkhaniyi chifukwa ali ndi owayimilira.
Iwo anapempha bwaloli Kuti awatulutse Mayi Patricia Kaliati pa belo kapena popanda belo.
Oyimira boma pa mlanduwu, a Levson Mangani auza bwalo la milandu kuti kupatula mboni zomwe zilipo, alinso ndi maumboni ena monga zoyankhurana pa lamya, komanso ma report a ndalama, mwa zina.