Khonsolo ya Mzuzu ikulephera kuchotsa ogulitsa malonda malo oletsedwa

Advertisement
Mzizu

Khonsolo ya mzinda wa Mzuzu yavomereza kuti yakanika kuchotsa anthu ogulitsa malonda m’malo osavomerezeka.

M’neneri wa khonsoloyi, McDonald Gondwe, wati khonsoloyi yalephela kusamutsa amalondawa, ndipo wati anthuwa, omwe amachitira mabizinesi awo m’malo osaloledwawa mu mzindawu, ambiri mwa iwo amabwerela m’malowa ngakhale kuti khonsoloyi ili ndi njira zambiri zoyendetsera zinthu pofuna kuthana ndi mchitidwewu.

“Tsopano tikulingalira zopeza yankho lachikhalire komanso tikulumikizana ndi mabungwe osiyanasiyana kuphatikiza mavenda kuti tigwirizane kupeza yankho limodzi,” watero Gondwe. 

Iye wadandaula kuti chiwerengelo cha anthu omwe akuchita malonda mbali mwa m’misewu yamzindawu chikukula kwambiri.

Gondwe watinso: “Tili ndi Msika mkatikati mwa mzinda, msika wa Zigwagwa ndi msika wa Ndata [mwe udayamba kugwira ntchito m’chaka cha 2014 koma ngakhale malowa alipo, mavenda ena amakonda kukagulitsira malonda awo m’malo osavomerezeka.” 

M’modzi mwa mavenda omwe amagulitsa zinthu kunja kwa Msika waukulu Adam Ascot wati malonda amamuyendera bwino akakhala kuti akugulitsira kunja Kwa msikawu kusiyana ndi mkati mwa msika.

“Tikufuna a khonsolo akatiyike ku msika wabwino womwe ungatithandize kulimbikitsa malonda athu chifukwa sitikukhutira ndi komwe khonsoloyi ikufuna kutisamutsira.

“Pano pa tsiku, ndikumakwanitsa kugulitsa katoni imodzi ya sopo, pomwe zitha kunditengera masiku atatu kapena anayi kuti ndigulitse katoni ngati yomweyi pa msika wa Ndata Flea,” watero Ascot. 

Wogulitsa wina, Jane Soko yemwe amagulitsa mbatata pamalo omwe ndiosavomerezeka walimbikitsa khonsoloyi kuti ikulitse msika waukulu kuti malo achuluke kuti mavenda ambiri azitha, kugulitsa m’malowo.

Wachiwiri kwa mlembi wa msika wa Central, Master Katete walimbikitsa khonsoloyi kuti ipeze njira yothetsera vutoli kuti aliyense poika njira zomwe zipangitse kuti ochita malonda azipindula komanso khonsolo izipindulaso.

Advertisement