Kubwera khwimbi ku UTM – watelo Kabambe

Advertisement
Malawian Economist Dalitso Kabambe is aspiring for president

Dalitso Kabambe yemwe wangolowa kumene United Transformation Movement (UTM) kuchokera ku chipani cha Democratic Progressive (DPP), wati chipanichi chiyembekeze kuti chilandira alendo ankhaninkhani kuchokera ku zipani zina.

Kabambe yemwe adali mkulu wa kale wa banki yaikulu ya Reserve wayankhula izi pomwe lero walandilidwa mchipani cha UTM kudzera pa msonkhano omwe wachitika pa Masambanjati m’boma la Thyolo.

Iwo ati ndi okondwa kuti tsopano alowa chipani cha UTM chomwe ati chili ndi mfundo zogwira mtima komanso anthu a chikondi omwe awalandira mopatsa kaso.

Kabambe wati, “M’mene mwandilandira ine, muyembekezere chikhamu cha anthu kulowa chipanichi. Ine ndaona mfundo ndi malamulo a zipani zambiri m’dziko mumo koma yomwe zinandigwira mtima ndi za UTM. Chaka cha mawa a Malawi akufuna kusintha, aone zina.”

Mlembi wa chipani cha UTM Patricia Kaliati wati awalandira a Kabambe ndi manja awiri ndipo awalimbikitsa kuti amasuke kuthandiza chipanichi kupititsa patsogolo masomphenya ake ponena kuti, “Changa changa chinavundira pa nsalu.”

Sabata yatha a Kabambe anatutumutsa anthu pomwe analengeza kuti atuluka chipani chotsutsa boma cha DPP komwe anali ataonetsa kale chidwi chokapikisana nawo paudindo wa mtsogoleri wa chipanichi ku konveshoni yomwe ichitike mwezi wa mawa.

Advertisement