Khonsolo yati malo amabasi atsopano ku Lilongwe ndiongoyembekezera chabe

Advertisement
Bus Terminal

Pomwe anthu ochuluka makamaka m’masamba a nchezo akuselewura komaso kunyogodora malo okwelera ndi kutsikira mabasi munzinda wa Lilongwe, khonsolo ya mnzinda wu yati malowa ndipongoyembekezera chabe.

Izi zikubwera pomwe posachedwapa khonsolo ya mnzindawu inalamura kuti mabasi akuluakulu onse kuyambira lero Lolemba, pa 24 June 2024 ayambe kugwilira ntchito zake pa Grand Business Park pomwe pamangidwa misasa ingapo ya anthu odikilira kukwera mabasi.

Potsatira zithuzi zomwe zikuzungulira m’masamba a nchezo zomwe zikuonetsa misasayi pa malowa, anthu ambiri asonyeza kusakondwa ndi malo okwelera bus-wa ponena kuti sakuoneka mwadongosolo kuti ma bus kuphatikizapo opita ndi kuchokera mayiko akunja angayambe kugwilirapo ntchito yotenga ndi kusiya anthu.

Pa ndemanga zina zomwe taona pa tsamba lina pa fesibuku, Idrah Kidi wati, “Izitu zopusa kwambiri. Ku Blbus depot ngati kotaya zinyalala. Mukatero muziti mwawononga ma millions apa.”

Koma khonsolo ya mnzinda wa Lilongwe itawona zina mwa ndemanga za anthu zokhudza malowa, yatulutsa kalata momwe yafotokoza kuti malowa ndipongoyembekezera chabe.

Mukalatayi nkulu wa khonsoloyi Macloud Kadam’manja wati, “khonsolo ya mzinda wa Lilongwe (LCC) yamva madandaulo pankhani yolamura mabasi kuti asamukire ku Grand Business Park ngati njira yongoyembekezera yobweretsera bata mu mzindawu pankhani yoyimitsa magalimoto makamaka mabasi akuluakulu.

“Tikudziwitsanso anthu onse kuti mpaka pano khonsoloyi siyinagwiritsepo ndalama iliyonse pa zomwe tapangana ndi eni ake a Grand Business Park popeza malowa adaperekedwa ku khonsoloyi kwaulere.”

Potsatira ndemanga zomwe anthu atulutsa zokhudza malo okwelera mabasiwa, khonsoloyi yati masana lero Lolemba, pa 24 June 2024, ichititsa nsonkhano wa atolankhani kuti ifotokozere bwino zankhaniyi.

LCC yati pa nsonkhano wa atolankhaniwu, ifotokozaso tsatane tsatane wa zinthu zonse zomwe zikuchitika pakadali pano pa lingaliro lake lokoza malo okwerera mabasi amakono.

Advertisement

One Comment

Comments are closed.