Kamlepo watuluka pa belo, m’busa wina wamangidwaso

Advertisement
Kamlepo Kalua

Pomwe phungu wa nyumba ya malamulo ku m’mawa kwa boma la Rumphi a Kamlepo Kalua watulutsidwa pa belo lero, apolisi amangaso m’busa wa mpingo wa CCAP pamlandu okhudza kufalitsa za ngozi ya ndege yomwe inapha wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino a Saulos Chilima ndi anthu asanu ndi atatu.

Wofalitsa nkhani za apolisi m’dziko muno Peter Kalaya, ndi omwe atsimikizira nyumba zina zosindikiza nkhani m’dziko muno kuti a Kalua omwe anamangidwa Lachinayi sabata yatha, atulutsidwa pa belo Lolemba masana.

A Kalaya ati ngakhale a Kalua atulutsidwa, apolisi apitilira kuchita kafukufuku pa mlandu womwe akuwaganizira kuti anafalitsa nkhani zonama pa masamba anchezo.

Wofalitsa nkhani za apolisiyu, watsimikizaso kuti apolisi amanga m’busa Kondwani Chimbirima Gondwe wa mpingo wa CCAP ku Zolozolo munzinda wa Mzuzu pa mlandu ofanana ndi womwe a Kalua akuganizilidwawu.

M’busayu wakhala wachitatu kumangidwa mokhudzana ndi ngozi ya ndege kamba koti sabata yatha a Kalua anamangidwa limodzi ndi a Bon Kalindo.

Onsewa akuwaganizira kuti anagawa pa masamba anchezo uthenga omwe uli ndikuthekera kusokoneza dziko lino okhudza ngozi ya ndege yomwe inapha wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino malemu Saulos Chilima pa 10 June chaka chino.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.