Wachi Yao, Sewa K, atulutsa nyimbo yatsopano ya hip-hop ‘Noo Noo’ 

Advertisement
Sewa K

Msungwana oyimba za ma lapulapu (hip-hop) muchi yao yemwe amakhala ku South Africa yemwenso ndi wakwathu konkuno Sewa Kalanje, lodyera Sewa K watulutsa nyimbo dzina lake Noo Noo.

Sewa wati nyimbo imeneyi ikukamba maka za umoyo wamasiku ano m’mene anthu timakhalila kuweluzana pazomwe mzako sali. 

“Ena amakonda kuweluza amzawo pomaziona kuti Iwo ndiwolungama pazochitika monga mavalidwe ndi zina pomwe iwowonso ali ndizawo zomwe amachita zosemphana ndi mawu a Mulungu,” watero Sewa

Oyimba yemwe kumudzi kwawo ndi ku Mangochi anayamba kuyimba mu 2010 koma wadziwika bwino chaka chino atatulutsa nyimbo yatsopanoyi masiku atatu apitawa imene yamukwanitsira nyimbo zisanu zake zoyimbidwa muchi yao. 

“Ndinabadwira ku Mangochi kwawo kwa a Yao ngakhale kuti sindinakulire kumeneko koma ndimakondabe mtundu wanga, wachiyao wangalusa,” anadzitukumula Sewa. 

Nyimbo ya Noo Noo yomvera wajambula ndi Tricky Beats mothandizana ndi Foxy G, pomwe ya kanema yajambulidwa ndi Hesi.

kumapeto kwake Sewa wathokoza a Malawi chifukwa cha sapoti apeleka ndipo wawamema kuti mupitilize.

Advertisement