Anthu oyenda maulendo a pakati pa Lilongwe ndi Blantyre tsopano adzikhala ndi chisankho cha mayendedwe awo pomwe boma lalengeza kuti maulendo a sitima yapamtunda ayambiraso pakati pa mizinda iwiriyi.
Izi ndi malingana ndi nduna yowona za mtengatenga ndi mtokoma a Jacob Hara omwe anena izi Lolemba munzinda wa Lilongwe.
A Hara ati nkhaniyi ikutsatira kukonzedwa kwa maulalo awiri omwe anawonongeka m’buyomu ndipo akhala akulepheletsa sitima ya pamtundayi kuchoka ku Blantyre kukafika ku Lilongwe.
Ndunayi yatsindika kuti ntchito yokonza maularowa ili ku mapeto ndipo pakamatha sabata zitatu, sitima za pamtundazi zikhala zitayamba kuyenda pakati pa mizinda iwiriyi.
Iwo awonjezeraso kuti unduna wawo ukupanga chothekera kuti ukozenso njanji yochoka munzinda wa Lilongwe ndi kukafika kuchipata cha m’boma la Mchinji.
Iwo ati izi zithandizira kukonzanso mavuto amayendedwe m’dziko muno zomweso ati zitha kuthandizira kupititsa chuma cha dziko lino patsogolo molinganaso ndi masomphenya a Malawi 2063.
Malingana ndi mkulu wa kampani ya Central East African Railways a CM Singh, mwezi wa mawa maulendo a sitima za pamtundazi ayamba ndi sitima zonyamula katundu, kenaka mtsogolomu sitima zonyamula anthu ziyambaso.