Nzika ya ku Niger ayikaniza Belo

Advertisement
Malawi24

Mzika ina ya m’dziko la Niger yomwe anaimbwandila lachiwiri pa bwalo la ndege la Kamuzu  mu mzinda wa Lilongwe ipitilira kuyankha mulandu wake opezeka ndi makhwala owopsya ku malo ochitila chimbudzi mawa atayikaniza belo. 

Mzikayi yomwe dzina lake ndi Osman Mohamed wa zaka 30 ayikaniza belo itakaonekela ku bwalo la milandu la Mkukula ku Lumbadzi pa mulandu opezeka komanso kufuna  kuzembetsa mankhwala owopsya ozunguza bongo otchedwa Diamorphine. 

Malinga ndi ofalitsa nkhani wa apolisi ya ku bwalo la ndenge la Kamuzu International Airport (KIA), a Sapulain Chitonde, nzikayi idapezeka ndi mapakete 51 omwe adawabisa mzikwama zawo ndi ena okwana 13 adali ku malo ochitila chimbudzi pa nthawi ya chipikisheni. 

Apolisi pa KIA ati anaipatsa nzikayi madzi akumwa otentha kuti achite chimbudzi chokakamiza ndipo inakwanitsa kutulutsa mibulu 13 ya mankhwalawa. 

Mzikayi inali pa ulendo wake opita m’dziko la Germany ndipo pa nthawi yogwidwayi amayembekezereka kukwera ndege ya Ethiopian Airlines.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.