Khonsolo ya mzinda wa Zomba yalimbikitsa anthu kuchita masewero olimbitsa thupi

Advertisement
Zomba City Council

Khonsolo ya mzinda wa Zomba yalimbikitsa anthu okhala mu mzindawu kuti adzichita masewero olimbitsa thupi popeza amathandiza kuti thupi lidzikhala la mphamvu komanso losadwaladwala.

Wofalitsa nkhani ku Khonsolo ya mzindawu Sylvia Thawani ndiyemwe wayankhula izi ku Gymkhana Club pomwe khonsoloyi idachititsa masewero olimbitsa thupi (aerobics) komanso mpira wamiyendo ndi wamanja mogwirizana ndi a silikari ankhondo a Changalume Barracks. 

Thawani adati iwo adapanga ubale ndi a silikari ankhondowa kuti adzichititsa masewero olimbitsa thupi kamodzi pamwezi uliwonse pofuna kuti anthu okhala mu mzindawu azitenga nawo mbali pankhani yolimbitsa matupi awo.

Iye wapempha anthu kuti adzibwera mwa unyinji kudzatenga nawo mbali pazochitikazi monga mpira komanso aerobics popeza zonsezi ndizawulele.

“Tikufuna kuti anthu okhala mu mzinda wa Zomba matupi awo adzikhala amphamvu komanso osadwala dwala ndichifukwa chake tayamba kumachititsa masewero olimbitsa thupi,” a Thawani.

Mawu ake, m’modzi mwa anthu ochititsa masewerowa yemwenso ndi msilikari wa Changalume Barracks, Maxwell Muyaluka, adathokoza akulu akulu a Khonsolo ya mzindawu komanso akulu akulu a ku Changalume chifukwa chopanga ubale okuti adzichita masewero olimbitsa thupi pamodzi ndi mzika zokhala mumzindawu.

Muyaluka walimbikitsa abambo, amai komanso ana kuti adzibwera kudzachita nawo masewero osiyana siyana olimbitsa matupi awo popeza izi zimathandiza kuti asamadwaledwale.

Advertisement