Ndinakadziwa sinkanapanga, tikhululukileni aMalawi – wanong’oneza bondo Mtambo, Kaliati

Advertisement
Timothy Mtambo

Pomwe ntchito yofuna kudzigulira malo m’mitima ya a Malawi yafika mlingo wina, Timothy Mtambo wati anakadziwa kuti zidzakhala chonchi, sanakapanga zionetsero zomwe zinathandiza m’gwirizano wa Tonse kutenga boma, ndipo naye Patricia Kaliati wapepesa a Malawi pa malonjezo osakwanilitsidwa.

A Mtambo omwe ndi wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani cha Alliance For Democracy (AFORD), ayankhula izi lamulungu pa 19 May 2024, pa bwalo la masewero la Mponela m’boma la Dowa komwe chipanichi chinachititsa nsonkhano waukulu.

Iwo anauza khwimbi lomwe linasonkhana pa bwaloli kuti ndiokhumudwa kwambiri kuti zomwe iwo pamodzi ndi akuluakulu ena a m’gwirizano wa Tonse ankalonjeza, sizikuchitakabe mpaka pano pomwe padutsa zaka zinayi chilowereni m’boma.

Patricia Kaliyati -Zomba rally
Pepani aMalawi – Kaliati.

Apa mkuluyu anatchula lonjezo la feteleza otsika mtengo komaso kulemba achinyamata ntchito ngati ena mwa malonjezano omwe sakukwanilitsidwabe ndipo anenetsa kuti anakadziwa kuti zidzatele, sanakathandizira mgwirizanowu kutenga boma. 

“Ndikupepesa kwa mtundu wa a Malawi chifukwa zimene tinakulonjezani sitinakwanilitse. Tinanena zantchito koma palibe, za feteleza otchipa koma palibe, za ngongole koma ndiizo zikungopita kwa anthu amodzimodzi, anthu akuchipani. Ndiye zimenezi tikuti pepani.

“Ine ndimalakalaka ndikanakhala m’neneri kapena sing’anga oti ndizitha kuona ku tsogolo. Ndinakakhala ndinaona ku tsogolo komwe tikupita ndinakanena kuti chikho chimenechi chindipitilire. Izi ndikunena osaopa wina aliyese, ndikunena kuchoka pansi pa mtima wanga kuti zinthu zinalakwika,” watelo Mtambo.

Pa nsonkhano wina omwe chipani cha United Transformation Movement chinapangitsa m’boma la Zomba Lamulungu lomweli, mlembi wa chipanichi a Patricia Kaliati nawonso anapepesa kwa a Malawi ati kamba ka malonjezo omwe sanakwanilitsidwebe mpaka pano.

A Kaliati anauzaso anthu kumeneko kuti; “Tinkanena kuti anthu adzadya katatu ndi Ife, omwe ananena za ma mega farm ndi Ife, Tikuvomela kuti ndi Ife, omwe tinkati feteleza mudzagula wotchipa. Tikuti pepani, wapakaliyala samaimba beru.”

Advertisement