Mgwirizano ndi DPP ndiotheka – Mtambo

Advertisement
Timothy Mtambo Malawi

Mtsogoleri wa gulu la Citizens For Transformation (CFT), a Timothy Mtambo ati ndiokonzeka kugwilira ntchito limodzi ndi Democratic Progressive Party (DPP), chipani chimene anatengapo gawo kuti chichoke mu ulamuliro wa dziko la Malawi mu chaka cha 2019. 

A Mtambo amayankhula izi pa wayilesi ya Zodiak mu pologalamu ya padera yomwe yaulutsidwa Lachiwiri pa 7 May, 2024 momwe wanenena kuti chipani cha MCP chalephera kusitha nyengo za dziko lino ndipo ulamuliro wake watsala ndi masiku owerengeka . 

“Ngati zinthu zipitilize kuyenda mmene zilili pano, ndithu boma ili lichoka. Zimene tinkafuna sizinatheke, mavuto tinkawaona aja akuonekabe pano,” anatero Mtambo. 

Ngakhale Mtambo akudzudzula ulamuliro wa Tonse, wanenetsa kuti iye sakuona vuto lili lonse pa zionetsero zomwe anachititsa mu 2019 komaso 2020 zomwe zinathandizira kuti mgwirizano wa Tonse upambane pa chisankho cha chibwereza. 

“Kupanga zionetserozi ndi ufulu ndipo ngati pangakhale china chimene tichione kuti titenge njira imeneyo, titha kupanga zionetsero ndipo palibe amene angatiletse chifukwa ndi ufulu wathu,” anawonjezera choncho Mtambo. 

Mu pologalamu yomweyi, Mtambo watsimikizaso kuti gulu lake la CFT lalowa m’gwirizano ndi chipani cha Alliance For Democracy (AFORD) ndipo akuti mgwirizanowu ndiwofuna kutumikira a Malawi. 

Ngakhale anatsutsa mphekesera zomwe zinaveka kuti anapita kukakumana ndi akuluakulu a chipani cha DPP kuti akhale pa mgwirizano, Mtambo wati ngati DPP ikufuna kutumikira a Malawi ndi kugwirizana ndi mfundo za CFT, mgwirizano utha kutheka.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.