Khama lipindura: Mneneri Habakkuk yemwe, pafupipafupi, wakhala akupempha Shepherd Bushiri kuti amuthandize ndi K1 miliyoni yokha, waona ngati kutulo pomwe wapatsidwa K6 miliyoni ndi mneneri nzakeyu.
Habakkuk yemwe dzina lake lenileni ndi Stanford Sinyangwe, sadzayiwala tsiku La mulungu pa 5 May, 2024 kamba koti mneneri Bushiri anamuchitira chinthu chomwe wakhala akumupempha.
Patsikuli, Bushiri amachititsa mapemphero ku BICC munzinda wa Lilongwe ndipo atazindikira kuti mneneri Habakkuk, yemwe anatchuka kwambiri ndi ma kanema ansangulutso, ali mkachisi momwemo anamuitana kuti apite kutsogolo.
Habakkuk atafika ku tsogoloko, anati linali khumbo lake kuti pomwe anafika ku mapempheroko ayankhulane ndi Bushiri mwapaderadera. Mneneriyu, yemwe amachokera ku Nselema m’boma la Chitipa, anati anali okondwa kwambiri kuti khumbo lake lokumana ndi mneneri nzakeyo lakwanilitsidwa.
Apa Bushiri anapempha munthu m’modzi odzipereka m’kachinsimo kuti awapase a Habakkuk ndalama zokwana 1000 ya m’dziko la America yomwe kwathu kuno ndi pafupifupi K2 miliyoni.
Poti tsiku lako likafika limakhala lafika; m’malo mwa munthu m’modzi panapezeka anthu okwana atatu odzipereka kupatsa Habakkuk ndalama yokwana K2 miliyoni aliyense. Izi zikutanthauza kuti Habakkuk watuluka mkachisimo ali ndi K6 miliyoni.
Mneneri Habakkuk anagwada pansi ndi chimwemwe chodzadza tsaya kuthokoza mneneri Bushiri kamba koti analowa mkachisimo ali khwakhwakhwa koma watuluka ali ndi mamiliyoni.
Mbuyomu Habakkuk wakhala akupanga ma kanema momwe amamupempha Bushiri ndalama yokwana K1 miliyoni yomwe amati amafuna adzilipilira nyumba yomwe amakha komaso kugulira zinkuza mawu zogwilitsa ntchito polalikira.
Nkuluyu anayamba kutchuka chaka cha 2022 kamba ka kanema yemwe anapanga momwe amapempha anthu kuti adzimupemphelera ponena kuti mtsikana wina anawabera ndalama zokwana K3000 ndipo ankati akudutsa muzowawa.
Chaka chatha, Habakkuk anagwedezanso kwambiri masamba a nchezo kamba ka kilipi ina momwe ankayankhulana ndi mzimayi wina yemwe mwa nthabwala anamuyimbira foni mtumikiyu kumuuza kuti wagwa naye mchikondi.
Mukilipiyo (audio clip), Habakkuk yemwe akuti ndi mwini wake wa mpingo wa Prophetic Ministries, anamuuza nzimayiyo kuti apeleke kaye ndalama yokwana K10,000 ngati akufunadi kumanga naye banja.