Kwabuka kusamvana ku NONM pa zionetsero

Advertisement
Nurses-doctors Malawi

Kwabuka kusamvana pakati pa anamwino ndi azamba pomwe mamembala a bungwe la National Organization of Nurses and Midwives of Malawi (NONM) akonza zokatseka ofesi ya bungweli Lachisanu ku Lilongwe ndipo akuloza chala atsogoleri a bungweli polepheletsa zionetsero zomwe zimayenera kukhalako lero iwo osawafotokozera bwino.

Nkhaniyi ikubwera pomwe sabata yatha, bungwe la NONM mogwirizana ndi bungwe la Physicians Assistants Union of Malawi (PAUM), analengeza kuti anamwino, azamba komaso ma kilinala akhala akuchita zionetsero lero Lachinayi m’dziko muno.

Malingana ndi kalata yomwe ma bungwe awiriwa anatulutsa sabata yatha, zionetserozo ndi kamba koti boma la Malawi kudzera ku unduna wa zaumoyo sunawayankhe pa pempho lawo loti akwezeledwe ndalama ya ma alawansi.

Koma pomwe anamwino, azamba ndi makilanala m’zipatala zonse za boma m’dziko muno anakozekera kuti lero akhala ali pansewu, NONM ndi PAUM yayimitsa kaye zionetserozi.

Kulepheretsedwa kwa zionetserozi, kukutsatila nsonkhano omwe akuluakulu a ma bungwe awiriwa anali nawo pamodzi ndi nduna ya zaumoyo a Khumbize Kandodo Chiponda Lachiwiri pa 30 April, 2024 ku Lilongwe.

Komatu ma membala angapo a bungwe la NONM omwe tayankhula nawo ndipo anapempha kuti tisawatchule mayina, atiuza kuti bungwe lawoli, lapanga chiganizo cholepheletsa zionetserozi osawafusa iwo kuti apeleke maganizo zomwe akuti ndizolakwika kwambiri.

Anthuwa atiuza kuti aka sikoyamba kuti atsogoleri a bungwe la NONM apange ziganizo zokayikitsa ndipo atiuza kuti pano mamembalawa agwirizana kuti mawa Lachisanu pa 3 May, 2024, agwirizana kuti akatseke ofesi ya bungweli ku Area 15 munzinda wa Lilongwe.

“Ndife achisoni ndi ganizo la atsogoleri a NONM poyimitsa mwadzidzidzi komaso pazifukwa zosamveka zionetsero zomwe zidakonzedwa. Utsogoleri sunafunse mamembala ake asanayimitse zionetserozi. Pamsonkhano wa NONM, PAUM ndi nduna ya zaumoyo, sizinakambidwe kuti zionetserozi ziyimitsidwe.

“Ndizodabwitsa kuti utsogoleri wa NONM udaganiza zoyimitsa zionetserozi poyerayera. Utsogoleriwu wapusitsa mamembala ake ndipo ndipamene tagwirizana zokatseka ma ofesi a bungwe la NONM kenaka kuyamba m’bindikiro sabata yamawa Lolemba,” watiuza choncho m’modzi mwa mamembala a NONM.

Poyankhula ndi tsamba lino za nkhaniyi, wachiwiri kwa mtsogoleri wa NONM Hannah Mtemang’ombe, watiuza kuti sakudziwa kanthu zoti ma membala awo ena akukonza zikatseka ofesi komaso kuchita m’bindikilo.

Iwo ati ndiodabwa kuti mamembala awo ena akuti sanauzidwe za zizifukwa zomwe bungweli lalepheretsera zionetserozi ponena kuti chili chonse chomwe chimachitika chokhudza nkhaniyi akhala akuwauza ma membala awowa kuphatikiza zonse zomwe anakambirana ndi anduna.

“Ofesi yanga siinalandire nkhani yoti ena akufuna kukatseka ofesi. Zionetserozi zalephereka chifukwa anduna atiuza kuti akonza mavuto athu pasanathe sabata ziwiri, nde nanga olo mutakhala inu mungapitilirebe kupita ku nsewu?

“Ife zonse zomwe zikuchitika tikumawauza ma memambala athu kuphatikiza zomwe takambirana ndi unduna. Ife ndife okhutira ndichiganizo chomwe tapanga choimitsa kaye zionetserozi,” watelo Mtemang’ombe.

Iwo akumbutsa mamembala a bungweli kuti m’gwirizano wawo ndi bungwe la Malawi Human Rights Commission (MHRC) umalimbikitsa kutsogoza zokambirana pakakhala vuto zomwe akuti ndi zomwe anapanga pokumana ndi a nduna a zaumoyo.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.