Bishop William Mchombo amukhazikitsa Lamulungu kukhala Bishop wa Anglican Diocese ya Upper Shire

Advertisement
Anglican Diocese

Mwambo okhadzikitsa Bishop William Mchombo kukhala Bishop wachitatu wa Anglican mu Diocese ya Upper Shire uchitika Lamulungu pa 26 May ku St Peters and Paul Cathedral Boma la Mangochi.

Wapampambo wa komiti yomwe ikuyendetsa zokonzekera mwambowu a Winasi Boma ati zonse zikuyenda bwino ndipo ali ndichikhulupiliro kuti mwambowu udzakhala wapamwamba.

Mtsogoleri wadziko lino a Lazarus Chakwera ndi akulu akulu ena a boma akuyembekezeka kudzakhala nawo pamwambowu.

Iwo atinso ma Bishop a mpingo wa Anglican ochokera m’maiko osiyana siyana monga Zambia, Zimbabwe, Botswana komanso Mozambique adzakhala nawo pamwambowo.

Wampampandoyu wapempha azipembedzo zosiyana siyana kuti adzabwere ku Mponda’s ndikudzakhala nawo pamwambo okhadzikitsa bishop watsopanayu. 

“Zokonzekera zonse zamwambowu zikuyenda  bwino ndipo nditsimikizire mtundu wa a Malawi kuti m’tsogoleri wadziko lino a Lazarus Chakwera adzakhala nawo patsikuli,” atero a Boma.

Bishop Mchombo akadzamukhazikitsa, adzakhala Bishop wachitatu wa Anglican mu Diocese ya Upper Shire ndipo akulowa mmalo mwa Bishop Brighton Vita Malasa yemwe adapuma pa udindowu.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.