Loya wanjatidwa kamba kogula galimoto yobedwa ku South Africa


Loya wanjatidwa kamba kogula galimoto yobedwa ku South Africa- Malawi24

Katswiri pa nkhani za malamulo a Stanley Chirwa omwe amayimilira anthu pa milandu, ali m’manja mwa apolisi powaganizira kuti anagula galimoto yomwe inabedwa m’dziko la South Africa ndi zigawenga zokhala ndi mfuti.

Ofalitsa nkhani za a Polisi m’dziko muno, a Peter Kalaya, ndi omwe atsimikiza za nkhaniyi ponena kuti a Chirwa amangidwa kumapeto kwa sabata yatha pomwe akuganizilidwa kuti anagula galimoto ya mtundu wa Ford Ranger.

A Kalaya awauza nyumba zina zofalitsa nkhani m’dziko muno kuti galimotoyi idabedwa ndi zigawenga za mfuti m’dziko la South Africa, m’chaka cha 2018.

Apolisiwa ati nkhaniyi yadziwika pomwe pa 8 April chaka chino, a Chirwa anapita ndi galimotoyi ku Road Traffic kuti akayilembetse ndipo uku nkomwe akuti anaizindikira kuti galimotoyi ikufanana ndi ina yomwe idabedwa ndi zigawenga m’dziko la South Africa.

Apa a Polisi anamufunsa katswiri wa za malamuloyu za komwe anatenga galimotoyi ndipo iye anasankha kusalankhura kanthu zomwe zapangitsa kuti a Polisi akhazikitse kafukufuku pa nkhaniyi yemwe anakali mkati.

Pakadali pano a Chirwa sanaonekerebe ku bwalo la milandu kuti awauze milandu yomwe akuzengedwa molingana ndi kupezeka ndi galimoto ya mtengo wapataliyi yomwe ili yobedwa.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading