Chipani chatsopano chalembetsedwa ku Malawi

Advertisement
Nzika Coalition

Pomwe chisankho chapatatu chaka cha mawa chino chikununkhira ngati mvula yogwa kutali, chipani chatsopano cha Nzika Coalition chalembetsedwa.

Chipanichi Lolemba pa 20 May chinali ku ofesi ya mkulu olembetsa zipani munzinda wa Blantyre komwe chalembetsedwa ndikupatsidwa makalata ochiyeneleza ngati chipani cha ndale tsopano.

Poyankhula ndi atolankhani atamaliza kulembetsa chipanichi, mtsogoleri wa chipanichi Christopher Mike Chiomba wati chipanichi chakhazikitsidwa ndicholinga chofuna kudzaombola a Malawi omwe wati ali pa mavuto adzaoneni.

Nzika Coalition
Tikufuna kuombola aMaawi – Nzika Coalition

Chiomba wati iwo ngati chipani akonzrkera bwino ndipo anenetsa kuti adzidilira kuti popanda mgwirizano ndi zipani zina atha kupambana chisankho chomwe chikubwera chaka chamawachi.

“Ife chipani chathu momwe timachiyamba tinalibe maganizo oti tidzapange mgwirizano ndi zipani zina chifukwa kumeneko nde kuti nd I kudzu yang wan its pansi.  Ife tili ndi chikhulupiliro chonse paife tokha,” watelo Chiomba.

Iwo ati chipani cha Nzika Coalition chikufuna kudzapanga zinthu zosiyana ndi zipani zonse ndipo mwa zina ati adzidzasankha nduna  zomwe sadzakhala anthu a ndale

Advertisement