Akhristu a St Charles Lwanga ndi St George ayenda njira yamtanda mogwirizana

Advertisement

Akhristu a Mpingo wa Katolika ku St Charles Lwanga Parish komanso akhristu a mpingo wa Anglican ku St George’s Parish mu mzinda wa Zomba lero ayenda njira yamtanda mogwirizana pokumbukira imfa ya Yesu Khristu.

Njira yamtandayi idayambira ku St George’s Anglican Parish mpaka kukafika ku St Charles Lwanga Roman Catholic Church ndipo idatsogodzedwa ndi a Vicar General ampingo wa Katolika Fr. Vincent Chilolo,  Fr Christopher Mizaya omwe ndi Archdeacon mumpingo wa Anglican komanso ansembe ena ambiri.

Akhristu mazanamazana kuchokera mipingo yonse iwiri adayenda nawo njira yantandayo kukumbukira imfa ija yapa mtanda ya Yesu Khristu.

Mu mau ake, Vicar General wampingp wa Katolika mu Diocese ya Zomba Fr Vincent Chilolo adapempha akhristu kuti adziwonetsa mtima wachikondi kwa anzawo momwe Yesu Khristu adawonetsa chikondi potifera ife pamtanda.

Fr Chilolo adapemphanso andale kuti adziwonetsa chikondi pakati pa anthu omwe akuwatumikira popeza anthu akuvutika m’dziko muno chifukwa andale alibe mtima wachikondi pakati pa anthu omwe akuwatumikira.

Akhristu amipingo yosiyanasiyana padziko lonse lapansi akukumbukira tsiku la Good Friday lomwe Yesu Khristu adatifera pamtanda pofuna kutipulumutsa machimo athu.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.