Akundikakamiza kuti ndipikisane nawo pa mpando wa upulezidenti, ndizotsutsana ndi chifuniro changa–Bushiri

Advertisement

Mtsogoleri wa mpingo wa Enlightened Christian Gathering (ECG), Prophet Shepherd Bushiri, wachenjeza anthu omwe akumema anthu m’masamba amchezo kuti apite munsewu kukachita zionetsero pofuna kukakamiza Mneneriyu kuti apikisane nawo pa udindo wa pulezidenti pa chisankho chapatatu chomwe chichitike chaka cha mawa m’dziko muno, ponena kuti asachite zoterezi popeza ndizosephana ndi chifuniro chawo.

A Bushiri anena izi kudzera pa tsamba lawo la mchezo la Fesibuku kutsatira zomwe anthu ena akuchita pomema anthu kuti akachite zionetsero m’misewu yadziko lino pofuna kuti mneneriyu apikisane nawo pa udindo wa pulezidenti.

“Ndaona pa malo ochezera a pa Intaneti kuti anthu apita kukachita ziwonetsero m’misewu ya kuno ku Malawi pofuna kundikakamiza kuti ndipikisane nawo pa udindo wa pulezidenti. Ndikuchenjeza mwamphamvu ndimonenetsa kuti tisachite zotere. Ndizotsutsana ndi chifuniro changa,” Watero Bushiri.

Naye katswiri panyimbo m’dziko muno amene amadziwika bwino ndi dzina loti Phungu Joseph Nkasa anayankhapo pa zankhaniyi kudzera mugawo la ndemanga ponena kuti a Bushiri wo ayima ndipo nyimbo walemba kale.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.