Aphungu adutsitsa chamba

Advertisement
Simplex Chithyola Banda

Mpungwepungwe unakula m’nyumba ya malamulo pamene mbali ya boma yavomereza lamulo kuti ulimi wachamba udzilimidwa m’dziko muno.

Izi zinadzetsa mpungwepungwe kunyumbayi pamene aphungu achipani chotsutsa cha Democratic Progressive Party (DPP) anati sakugwirizana ndi lamuloli.

Izi zinapangitsa aphungu achipanichi kutuluka pa zokambilanazi ati kusonyeza kusakondwa ndi lamulori.

Ngakhale aphunguwa anatuluka panja, nyumbayi inavomereza za biloyi ndipo ikhale lamulo ngati mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera asainile.

A Peter Dimba, yemwe ndi phungu wa nyumba ya malamulo wadera la kum’mwera m’boma la Lilongwe, ndi omwe anabweretsa bilo yoti alimi adzilima chamba m’dziko muno ponena kuti chambachi ntchito yake sikusuta ayi koma chizigwilitsidwa ntchito popangira zinthu zosiyanasiyana kuphatikizapo mankhwala zomwe zingathe kupititsa patsogolo chuma cha dziko lino.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.