Upepese, apo bii ndichita china chake – Zani Challe waopseza Tuno

Advertisement
Malawian Musician Tuno

…Tuno akuloza chala mowa omwe anamwa

Kuli chinkulirano pakati pa oyimba Zani Challe yemwe lero watulutsa chikalata chomuuza oyimba Tuno kuti amupepese apo bii apanga chinthu china chomwe sananene ati kamba komunena kuti iye amagulitsa thupi komaso amachita malonda a mankhwala ozunguza ubongo.

Nkhaniyi yayamba Lachiwiri usiku pomwe Tuno yemwe anabadwa Tunosiwe Mwakalinga amacheza mu pologalamu ya ‘Truth or Drink’ yomwe imaikidwa pa intaneti ndipo anavumbulutsa zina mwa zinthu zomwe zakwiyitsa Zani Challe.

Mwazina Tuno anati Zani Challe asiye kumanena kuti kunja komwe ali pano akuyimilira oyimba akazi mdziko muno ponena kuti kumeneko amapanga zinthu zosakhala bwino zomwe anati ndikuphatikizapo ku gulitsa thupi lake kwa azibambo osiyanasiyana.

Pomwe amapitilira kucheza mu pologalamuyi, Tuno anamutukwana Challe ati kamba komunena kuti iyeyo ndi Temwah samatha kuimba komaso kuti Tuno-yo akuti samatchena, ndipo apapa mpomwe anaonjezera kutsotsomora moto omwe watentha mtima wa Challe.

“Ngati wapita ku Nigeria bwanji sindinakuone ndi Tiwa Savege. Unapita ku Nigeria kukatani iwe, ungamatinene kuti ine ndi Temwa kuti sititchena f*? Nde komwe wapitako umakapanga chiyani kumeneko,” anatelo Tuno kwinaku akugwilidwa, kuletsedwa kuti asapitilize kuyankhula.

Kupatula apo, Tuno anamunena Challe kuti m’mayiko akunja omwe amapita amakachita malonda ogulitsa mankhwala ozunguza ubongo zomwe zikuoneka kuti ndi zomwe zakwiyitsa Challe kwambiri kufika potulutsa chikalata chomuopseza Tuno kuti apanga chinthu china.

Mu kalatayi, ngakhale kuti Zani Challe sanatchule Tuno, wati zomwe wayankhula Tuno zili ndi kuthekera komuipitsira mbiri yake choncho wamuuza kuti abweretse umboni pa zomwe wanenenazo kapena apepese pa gulu.

“Ndine wokhudzidwa kwambiri ndi khalidwe losayenera limene munthu wina wachita, makamaka pondinamizira zinthu, kuphatikizapo bodza loti ndimachita nawo zinthu zosayenera monga kugulitsa mankhwala osokoneza ubongo ndi ntchito zoperekeza anthu.

“Ndikulimbikitsa munthu uyu kuti apereke umboni weniweni wotsimikizira zomwe akunena kapena kupepesa pagulu. Kulephera kutero kuchititsa kuti ndi chitepo kanthu. Ndikofunika kuzindikira kuopsa kwa mawu achidani, ziwopsezo za nkhanza zakuthupi, ndi kunena zopanda pake, popeza siziyenera kuonedwa mopepuka,” yatelo mbali ina ya kalata ya Challe yomwe yalembedwa mchingerezi.

Iye wapitiliza ndi kunena kuti monga mkazi, akhulupirira kuti ndikofunikira kuchita zinthu mwa umunthu ndipo wati awonetsetsa kuti ateteze mbiri ndi ntchito zake, ndipo wati salora kuti zoneneza zopanda pake zochokera kwa munthu m’modzi zisokoneze kulimbikira kwake.

Challe asanatulutse kalatayi, Tuno anali atayamba kale kunong’oneza bondo pa zomwe anayankhulazo kamba koti m’mawa wa lero, analemba pa tsamba lake la fesibuku ndikunena kuti sali okondwa ndi zomwe anachita atamwa mowa mu pologalamuyi.

“Moopa mtima, sizindisangalatsa ndikamwa mowa, ndichizindikiro kuti mowa si mbali yanga, kutukwana kumene kuja ine ayiiiiii, nooo. Anandiputa, koma eish kutukwanako ndakutenga kuti???? Iyayi siine okondwa ndi zimenezo pokhala kholo komaso owopa Mulungu. Siine okondwa,” analemba chomcho Kuno pa tsamba lake.

Advertisement