Mayi wophwanya paipi yamadzi kuti atunge aulele walipira chindapusa cha K300,000

Advertisement

Mayi wa zaka 21 yemwe anamangidwa mkati mwa sabatayi chifukwa chophwanya mwadala paipi ya madzi a Blantyre Water Board ndicholinga choti atunge madzi aulele, amulipitsa chindapusa cha ndalama yokwana K300,000.

Malingana ndi ofalitsa nkhani pa polisi ya Limbe a Aubrey Singanyama, a Celina Ganya omwe akuti anapalamula mlanduwu Lachiwiri sabata ino pa 5 March, 2024 ku Bangwe munzindawu, anakaonekera ku bwalo la milandu Midima Third Grade Magistrate Lachinayi pa 7 March, 2024.

Singanyama wati mayi Ganya amayankha milandu iwiri; wina owononga katundu ndi wina opeza madzi kapena kuti kutunga madzi mwachinyengo ndipo mayiyu anaivomera milandu yonseyi.

Atafusidwa kuti apeleke dandaulo bwalo la milandulo lisanapeleke chigamulo chake, mayi Ganya anapempha bwalolo kuti liwapatse chilango chochepa ponena kuti ndikoyamba kupalamura komaso anati iwo ndi ophunzira wa form 4 ndipo akuyenera kulemba nawo mayeso a MANEB chaka chino.

Atamva pempholi, oweruza milandu Mtawali, anagamula kuti pa mlandu oyamba omwe ndikuononga katundu, mayiyu apeleke chindapusa K200,000 kapena akagwire ukaidi wa kalavula gaga kwa miyezi khumi ndi iwiri (12).

Pa mlandu wachiwiri omwe ndi kupeza madzi koma mwachinyengo oweruzayu analamura kuti mayi Ganya alipire chindapusa cha ndalama yokwana K100,000 kapena akagwire ukaidi wa kalavula gaga kwa miyezi khumi ndi iwiri (12) ndipo analamula kuti ngati mayiyu salipira zindapusazi, mayiyu akakhale kundende miyezi yonse 24.

Mayi Celina Ganya omwe ndiochokera m’mudzi mwa Ganya, mfumu yaikulu Ganya m’boma la Ntcheu, sanazengeleze ndipo tikukamba pano ndi mfulu kamba koti alipira kale chindapusa cha K300,000 yomwe agamulidwayo.

Lolemba pa 4 March, 2024, paipi ina ya Blantyre Water Board idasweka kotelo kuti madzi ankatuluka ndi kumangotayika zomwe zinapangitsa anthu okhala mdelari kuti azitunga madzi aulele kudzera pa paipiyi.

Lachiwiri chakumasana munthu wina wakufuna kwa bwino, anakoza paipi yoswekayo kotelo kuti madzi anasiya kutuluka zomwe zinakwiyitsa mayi Ganya omwe kenaka anaphwanyaso mwadala paipiyo kuti apitilirebe kutunga madzi aulerewo ndipo potsatira izi anamangidwa.

Advertisement