Apolisi awiri awachotsa ntchito ku Thyolo

Advertisement
Police

Nthambi ya apolisi dziko muno yachotsa ntchito apolisi awiri amene amagwira ntchito m’boma la Thyolo chifukwa cha kulephera kusunga mwambo komaso kujomba ku ntchito mopanda chilolezo.

Mu kalata yomwe wasainira ndi wachiwiri kwa mkulu wayang’anira antchito ku nthambiyi, Maxton Kalimanjira, ikufotokoza kuti apolisi awiriwa analephera kusunga mwambo komanso amachoka malo ogwirira ntchito mosatsatira malamulo.

Malinga ndi kafukufuku yemwe Malawi24 yapeza, akusonyeza kuti kositabo Chikumbutso Maluwa, kositabo Davie Mataya ndi wina amene sanatchulidwe dzina anachoka malo awo ogwilira ntchito pamene dipiti wa galimoto za tsogoleri wa dziko lino, Dr Lazerous Chakwera umadutsa kupita ku mwambo okumbukira M’busa John Chilengedwe omwe unachitika pa 15 January, 2024 m’boma la Chiradzulu.

Mkulu wa Bungwe lomenyera ufulu wa anthu la Centre for Democracy and Development Initiative (CDEDI), Sylvester Namiwa wati tsogoleri wa dziko lino, Dr Lazerous Chakwera akuyenera kulamula mkulu wa apolisi dziko muno kuti awunikeso kuchotsedwa kwa anthuwa ponena kuti boma likuyenera kuchepetsa apolisi omwe amakhala mphepete mwa msewu ukakhala kuti tsogoleri wa dziko lino ali ndi alendo

Advertisement