Bungwe lowona za akatswili pa ukadaulo wa makina a ma kompyuta ndi zipangizo za makono la ICT- Association of Malawi (ICTAM) lati lili lokozeka kuthandiza ndi ukadaulo udziwi wawo ku bungwe lowona za anthu otuluka ndi kulowa m’dziko muno la Immigration pamene pakali pano likukumana ndi mavuto popanga ziphaso.
Bungweli lati ilo monga bungwe lomwe cholinga chake mkufuna kuwonetsetsa kuti makono ano anthu akugwiritsa ntchito njira za makono kutukula chuma pa dziko lati likuwona mavuto amene nthambi ya Immigration ikudutsamo maka ku nkhani yodhinda zikalata zoyendela (passports) ndipo lati lilowelera kugwira ntchitoyi modzipereka monga nzika zokhudzika kuchotsa zotchija pa kudindidwa kwa ziphaso.
ICTAM Kudzela mwa mlembi wawo Andrew Kamwendo ati potengera zomwe mtsogoleri anayankhula m’nyumba ya malamulo poyankha mafunso a aphungu, midziwi pa ma kompyuta ili chile kuti ipange mgwirizanowu ndi Immigration kuthana ndi mavuto onse kuti zinthu zibwerere mchimake ndinso kuti chuma chipitilire kuyenda mdziko muno Kudzela m’maulendo.
Mtsogolero wa dziko lino Lazarus Chakwera mnyumba ya malamulo anati anthu ena achipongwe adaba njira zopangila ziphaso za ma ulendo ndi cholinga choti alipidwe ndalama zambirimbiri kuti abwezeretse njirayo.
Mtsogoleriyu adatsindika kuti boma silili lokonzeka kutaya ndalama mu anthu achipongwe ndipo ndipo anapeleka malire ku nthambi ya Immigration kuti iwonetsete kuti zonse zabwerera mchimake pasadathe ma sabata awiri.
Anthu ambiri mdziko muno ali kakasi ndipo ambiri akumakhalira ku nthambizi pamene akukanika kutenga ziphaso zawo zoyendera.