ICTAM yatasa dzanja pa bungwe la  Immigration

Advertisement
Malawi Immigration offices in Lilngwe

Bungwe lowona za akatswili  pa  ukadaulo wa makina a ma kompyuta ndi  zipangizo za makono  la ICT- Association of Malawi (ICTAM) lati lili lokozeka kuthandiza  ndi ukadaulo udziwi wawo ku bungwe lowona za anthu otuluka ndi kulowa m’dziko muno la Immigration  pamene pakali pano  likukumana  ndi mavuto popanga ziphaso.

Bungweli lati ilo monga bungwe lomwe cholinga chake mkufuna kuwonetsetsa kuti makono ano anthu akugwiritsa ntchito njira za makono kutukula chuma pa dziko lati likuwona mavuto amene nthambi ya Immigration ikudutsamo maka ku nkhani yodhinda zikalata zoyendela (passports) ndipo lati lilowelera kugwira ntchitoyi modzipereka monga nzika zokhudzika kuchotsa zotchija pa kudindidwa kwa ziphaso.

ICTAM Kudzela mwa mlembi wawo Andrew Kamwendo ati potengera zomwe mtsogoleri anayankhula m’nyumba ya malamulo poyankha mafunso a aphungu, midziwi pa ma kompyuta  ili chile kuti ipange mgwirizanowu ndi Immigration kuthana ndi mavuto onse kuti zinthu zibwerere mchimake  ndinso kuti chuma chipitilire kuyenda mdziko muno Kudzela m’maulendo.

Mtsogolero wa dziko lino Lazarus Chakwera mnyumba ya malamulo anati anthu ena achipongwe adaba njira zopangila ziphaso za ma ulendo ndi cholinga choti alipidwe ndalama zambirimbiri kuti abwezeretse njirayo.

Mtsogoleriyu adatsindika kuti boma silili lokonzeka kutaya ndalama mu  anthu achipongwe ndipo ndipo anapeleka malire ku nthambi ya Immigration kuti iwonetsete kuti zonse zabwerera mchimake pasadathe  ma sabata awiri.

Anthu ambiri mdziko muno ali kakasi ndipo ambiri akumakhalira ku nthambizi  pamene akukanika kutenga ziphaso zawo zoyendera.

Advertisement