Nyamata wazaka 19 wapha mzake polimbirana mkazi

Advertisement
Machinga

Nyamata wazaka 19 ku Chilipa m’boma la Mangochi ali m’manja mwa apolisi kaamba koti akuganizilidwa kuti wapha mzake chifukwa cholimbirana mkazi.

Woganiziridwayu yemwe dzina lake ndi Anusa Sausande adabaya ndikupha Kassim wazaka 21 zakubadwa pomwe adali kulimbirana mkazi.

Nkhani yonse ikuti Sauzande ndiyemwe adayamba kupalana ubwezi ndi mkaziyu ndipo pakutha pa nthawi ubweziwu udatha.

Apa mpamene Chilambe adagwa mchikondi ndi mkaziyo atadyera maso ndipo izi sizinasangalatse Sauzande.

Lamulungu lapitali Sauzande adapeza mamunayo akuchezetsa ndi mkaziyo. Apa Sauzande adatenga mpeni ndi kumubaya mamunayo pa chidale.

Anthu ena akufuna kwabwino anatenga Chilambe ndi kuthamangira naye kuchipatala cha Phirilongwe komwe anafa pomwe amalandira thandizo.

Malingana ndi achipatala ati Chilambe wafa kamba koti anataya magazi ochuluka kutsatira kubayidwako.

Pakadali pano mneneri wa apolisi m’bomali a Amina Tepani Daudi watsimikiza zakumangidwa kwa nyamatayu ndipo Sauzande akuyembekezeka kukawonekera ku bwalo la milandu posachedwa.

Advertisement