Katswiri pandale wati a Mutharika ayankhule zolimbikitsa umodzi

Advertisement
Malawi APM

M’modzi mwa akatswiri pandale m’dziko muno a Lyford Chadza, wati mtsogoleri wakale wa dziko lino a Peter Mutharika akuyenera kusamala pamene mtsogoleriyu wati ali ndi mau opita kwa mtsogoleri wa dziko a Lazarus Chakwera.

Katswiriyu wapempha a Mutharika kuti zomwe ayankhule zikhale zobweretsa umodzi pozindikila kuti zomwe iwo angayankhule zili ndi kuthekera kobweretsa umodzi kapena kuwonjezera mkwiyo pakati pa anthu otsatira zipani m’dziko muno.

Malawi APM
A Mutharika apemphedwa kuyankhula zomanga Malawi.

A Chadza anena izi kutengera ndi momwe nkhani zandale zikuyendera mdziko muno. Ndipo iwo apemphanso a Mutharika kuti mfundo zomwe a Mutharika ayankhule zikhale zomanga ndi kubweretsa umodzi.

A Mutharika akuyembezeka kuyankhula mau opita kwa mtsogoleri wa dziko lino lachitatu likudzali, kutsatira zachiwembu zomwe zidachitika pamalo omwetsera mafuta a Mbowe munzinda wa Lilongwe.

Advertisement