Bungwe loyendetsa zisankho mdziko muno, la Malawi Electoral Commission (MEC) lati anthu omwe ali ku Israel komanso mayiko ena akunja sadzakhala nawo mwayi oponya mavoti pa zisankho za patatu zomwe zidzachitike m’mwezi wa September chaka cha 2025.
Malingana ndi mneneri wa bungweli, a Sangwani Mwafulirwa, malamulo a dziko lino salola anthu omwe ali kunja kwa dziko lino kuponya nawo voti kudzera pa makina a intaneti kapena kudzera ku positi ofesi ngati momwe mayiko ena achitira kwa mzika zake zomwe zili kunja kwa dzikolo.
Iye anatinso anthu omwe akupita mdziko la Israel akuyenera kudzabwera kuno ku Malawi m’mwezi wa September kudzalembetsa kuti adzakhale nawo ndi mwayi ovota kotero adzafunikanso kubwera kuno kumudzi m’mwezi ngati omweu kuti adzathe kudzaponya nawo voti.
Pazokhudza anthu omwe ali ndi chidwi kudzayimira nawo pa chisankho koma ali kumayiko akunja, a Mwafulirwa anati malamulo amalora kuti munthu wina atha kumutengera zikalata zomuvomereza munthu kudzayima nawo pa zisankho (Nomination Papers) mkukamuperelanso koma chomwe chimafunika ndi choti mwini wakeyo asayinire.
M’mwezi wa September chaka cha mawa cha 202, a Malawi adzakhala akuponya mavoti pa zisankho za patatu.