Ng’amba ikhala ikupitilira sabata – atero a zanyengo

Advertisement
800 hectares Mega farm rehabilitation starts in Mangochi

Nthambi yoona za nyengo yati madera ambiri m’dziko muno maka mu chigawo cha kum’mwera ndi pakati, ng’amba ikhala ikupitilira kwa sabata imodzi kamba koti mphepo ya mvula ikuombera dziko la Tanzania.

Ngakhale izi chili chomwechi, mkulu wa nthambiyi, Dr Lucy Mtilatila ati anthu asadere nkhawa kamba koti mphepo ya mvulayi ikhala ikubwereraso m’dziko muno posachedwa.

Mu ulosi wa za nyengo ya mvula mene ikhalire  mu chaka chino, nthambiyi yachenjeza kuti madera ena m’dziko muno akhala ndi ng’amba pamene madera ena alandira mvula ya bwino kufikira kudzakolora.

Madela ambiri m’dziko muno anayamba kubzala mbeu zawo kumapeto kwa mwezi wa November chaka chatha ndipo kafukufuku akusonyeza kuti mbeu zambiri zakhala zikupserera ndi dzuwa kufikira kumayambiriro a mwezi  wa January chaka chino pomwe madera ambiri m’dziko muno anayamba kulandira mvula yochuluka.

Advertisement