Malipoti osatsimikizika akusonyesa kuti apolisi munzinda wa Blantyre amanga anthu awiri powaganizira kuti anali nawo mu gulu la anamalira omwe anatchingira nsewu mdipiti wa galimoto za mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera pa mphambano ya HHI ku Blantyre, koma ofalitsa nkhani za apolisi mdziko muno wati atitsimikizirabe ngati mphekeserazi zili zoona.
Lachisanu lapitali, kunali chifwilimbwiti pa mphambano ya HHI munzinda wa Blantyre pomwe anamalira ena omwe ananyamula thupi la munthu wina lomwe amakaliyika m’manda a HHI munzindawu, anayimitsa mwachipongwe mdipiti wa galimoto zopelekeza mtsogoleri wa dziko lino, a Chakwera.
Pa nthawiyi, a Chakwera anali akuchokera ku nyumba ya chifumu ya Sanjika ndipo amathamangira ku bwalo la ndege la Chileka komwe amafuna kukakwera ndege paulendo wawo opita mdziko la Democratic Republic of Congo komwe akuti ayitanidwa mwadzidzi ndi mtsogoleri wa dzikolo.
Anamalirawa anayimitsa mdipitiwu ndikuyamba kuimba nyimbo za chipongwe, amvekele; “Mbuye timenyereni nkhondo kulimbana ndi satana, ali ndi zida zowopsa,” kenaka nkudzayamba kuimba kuti; “waimabe waimabe waimabe” kwinaku atawunjikana pakati pa nsewu wa Magalasi, kuchititsa kakasi nzika yoyambayi yomwe siikanachitira mwina koma kudikira kaye kwa mphindi zingapo.
Lero Lachiwiri pa 23 January, 2024, anthu m’masamba anchezo akugawana lipoti lomwe likusonyeza kuti apolisi munzinda wa Blantyre amanga a Pearson Chimimba a zaka 48 ochokera m’mudzi mwa Magola mfumu yaikulu Njolomole m’boma la Ntcheu komaso a Hector Ndawala a zaka 38, ochokera m’mudzi mwa Katundu, mfumu yaikulu Chimaliro ku Thyolo.
Malingana ndi lipoti la apolisi lomwe tsamba lino laona, a Chimimba akuganizilidwa kuti ankayendetsa galimoto ya ntundu wa Nissan Diesel, nambala yake ZA 5906 yomwe akuti inatchinga nsewu pa mphambano ya HHI munzinda wa Blantyre pa nthawi yomwe a Chakwera ankafuna kudutsa.
Mbali inayi lipoti la apolisili lomwe likusonyeza kuti odandaula ake anali Assistant Superintendent Mervis Matikanya omwe ndi ofesala pa Blantyre Police, likusonyeza kuti bambo Ndawala akuganizilidwa kuti ndi m’modzi mwa anthu omwe anayambitsa kuponya miyala pa malowa.
Lipotili lomwe pakadali pano sitingatsimikize ngati lili lowona kapena ayi, likusonyezaso kuti apolisi alanda galimoto yomwe ankayendetsa bambo Chimimba ndipo akuti kafukufuku anakali nkati kusakasaka anthu ena omwe akukhudzidwa ndi chipongwe chomwe mtsogoleri wa dziko linoyu anachitilidwa pa tsikuli.
Koma titaimbira foni ofalitsa nkhani za apolisi mdziko muno a Peter Kalata kuti atitsimikizire za nkhaniyi, atiuza kuti nawoso adziwa za nkhaniyi kudzera pa masamba anchezo ndipo apempha kuti tiwapatse kaye nthawi kuti afufuze ngati izi zilidi chomwecho kapena ayi.