Mlandu wa Lester Maganga ulowanso mu bwalo mwezi wamawa


Oweluza Milandu ku bwalo lalikulu a Mzondi Mvula apeleka chitsogozo chakuti mulandu wa a Lester Maganga ukhala ndi masiku khumi ndi anayi (14) kuti umvedwe ndipo kuti oganizilidwawa akakhalebe akusungidwa m’manja mwa a chitetezo kufikila mtsogolo..

Mu kumvedwa kwa mulanduwu lero ku bwalo lalikulu mu mzinda Lilongwe a Lester Maganga akana kuti iwo si olakwa pa milandu yonse iwiri yomwe akuwaganizira.

Oweluza Mvula wati tsopano mulanduwu udzayamba kumvedwa kuyambila pa 13 February mpaka pa 7 March chaka chomwechino zonse zikakhala mchimake.

Oyimilira mbali ya boma pa Mlanduwu awuza bwaloli kuti potsatila kukana kwa a Maganga milanduyi iwo abweletsa mboni zokwana khumi ndi zisanu (15) ndipo iwo anawonjezera kuti mboni zonse zilipo.

A bwalo alamulanso kuti aboma atengele oganizilidwawa ku chipatala kuti akawayeze ku kalikonse kokhudza ubongo m’masiku asanu ndi awiri akudzawa kuti mulanduwu ukayamba usakhale ndi zosokoneza.

A Lester Maganga akuwaganizila kuti adapha a Allan Wittika chaka chatha, Ndipo a bwalo akhala akuwayimba mulandu wakupha komanso opezeka ndi futi komanso zopolopolo popanda chilolezo.