Likulu la ndende lasamutsidwira ku Lilongwe

Advertisement

Akuluakulu atsimikiza kuti tsopano likulu la nthambi ya ndende lasamutsidwa kuchoka ku Zomba lomwe ndi likulu lakale la dziko lino kupita ku Lilongwe.

Izi ndi malingana ndi kalata yomwe nthambi ya ndende yatulutsa yomwe wasainira ndi ofalitsa nkhani wake Senior Superintendent Chimwemwe Mike Shaba omwe ati likulu la nthambi layamba kugwilira ntchito zaka munzinda wa Lilongwe kuyambira pa 8 January, 2024.

A Shaba kudzera mu kalatayi ati likulu la nthambiyi tsopano likupezekera ku Area 14, munyumba ya Magalasi ku likulu la dziko linoku.

“Malawi Prisons Services ndiyokondwa kudziwitsa mbali zonse zokhudzidwa komanso mtundu onse wa aMalawi kuti lasamutsa likulu lawo kuchoka ku Zomba kupita ku Lilongwe ku Area 14 Magalasi House kuyambira pa 8 January, 2024.

“Makalata Onse tsopano atumizidwe kwa: Commissioner General for Prisons, National Prisons Headquarters, Private Bag A28, Lilongwe, Malawi, kapena pa imelo (Email) ya, [email protected],” yatelo mbali ina ya kalata kuchokera ku nthambiyi.

Izi zikudza pomwe boma linasamutsaso kale nthambi monga yoyendetsa chisankho ya Malawi Electoral Commission (MEC) komanso yowona zolowa ndi zotuluka, Department of Immigration and Citizenship Services kuchoka ku Blantyre kupita ku Lilongwe.

Magulu ena m’mbuyomu akhala akudzudzula boma pa chiganizo chosamutsa nthambizi ponena kuti izi zili ndikuthekera kopangitsa kuti chitukuko chikhale mnzinda wa Lilongwe okha.

Advertisement