Khoti la Euthini, m’boma la Mzimba lagamula Martha Chaula wa zaka 47, kukakhala kundende kwa miyezi 18 popezeka wolakwa pa mulandu wofuna kuba khanda.
Bwaloli linamva kuti mayiyu anachita izi pofuna kusangalatsa mamuna wake, yemwe wakhala akuuza mkaziyo kuti amuberekere mwana ngati akufuna kuti amumangire nyumba komanso kumuyambitsira mabizinesi osiyana siyana.
Bwaloli linamvanso kuti mayiyu amadziwa bwino kuti iyeyo ndi chumba kamba koti chibelekero chake chili ndi mavuto ena, kotero mayiyu anapempha nzake yemwe amakhala ku Nkhata-Bay ndikumufutokozera kuti iye sangathe kubereka kotero amupezereko mzimai yemwe ali ndi mimba ndipo kuti ali ndivuto loti sangathe kulera mwana.
Izi akuti zinathekadi ndipo mai Martha Chaula anayamba kulumikizana ndi Brandina Banda ndikumuza kuti iwo ali ndi bungwe lomwe limathandizidwa ndi azungu kotero kuti akufuna kuti amuthandizire kulera mwana wake akabadwa.
Malingana ndi umboni wa Brandina Banda, iye anati mai Chaula anamutumizira ndalama yoyendera kuchoka ku Nkhata Bay kukafika ku Euthini, ndipo iye atafika akuti analandilidwa bwino.
Brandina atabereka mwana mayiyo anawuza Brandina kuti abwerere ku Nkhata-Bay ndipo anapatsidwa ndalama zoti akayambire Malonda aja koma panthawiyi Brandna amakana ndipo amafuna kuti akamabwerera ku Nkhata-Bay apite ndi mwana wake.
Koma mai Chaula anawuza Brandina kuti azungu anyamuka ndipo akhala akufika posachedwa ndipo sakufuna kuti azamupeze chifukwa akazampeza ndiye kuti azunguwo asiya kuthandiza.
Brandina poti anali ndichikhulupiro ananyamuka kubwerera ku Nkhata-Bay koma monyinyirika. Ndipo mai Chaula anayamba kuyimbira lamya anzake kuwawuza kuti iye wabereka mwana ndipo izi zinabwitsa anthu ena omwe akumuziwa bwino mayiyo.
Umboni wakuchipatala wa mai Chaula atayetsedwa zinadziwika kuti mayiyo sangathe kubereka, ndipo sanakhelepo ndi pakati.
Woweluza mulandu Harrison Sitiki Atamva maumboni wonse anagamula mayiyo kuti akakhale kundende miyezi 18, ndicholinga chofuna kupereka phunziro kwa amai wena omwe angakhale ndi maganizo onga ngati amenewa.