Nthambi yoona za ngozi zogwa mwadzidzi m’dziko muno ya Department of Disasters Management Affairs (DoDMA) yati mabanja omwe ali ndikuthekera kogwira ntchito koma ndi a ulesi sazilandira thandizo la chimanga kuchokera ku Boma.
Wanena izi ndi Mlembi Wamkulu ku nthambiyi, Charles Kalemba, m’mudzi mwa mfumu yaikulu Tengani m’boma la Nsanje, pomwe adapita kukakambirana ndi adindo za tsogolo logwiritsa ntchito sikimu ya Ntolongo yomwe idamangidwa ndi nthambiyi ndi thandizo la ndalama zochokera ku African Development Bank pansi pa pulojekiti yobwezeretsa mchimake zinthu zomwe zinaonongeka ndi Namondwe wa Idai m’chaka cha 2019.
Kalemba wati nthambiyi isiya kupereka thandizo kwa anthu omwe apatsidwa mwai wodzidalira pawokha pa chakudya komanso pa miyoyo yawo koma sakuugwiritsa ntchito chifukwa cha ulesi.
“Tili odabwa kuti m’malo mogwiritsa ntchito sikimuyi yomwe ndi ya ma hekitala oposa 80, anthu m’dera la Gulupu Ntolongo akungoiyangána pomwe anzawo omwe anamangiridwa ma sikumu oterewa m’boma lomwelo akusimba lokoma pokolora katatu pachaka.
“Aliyense yemwe ali mgulu la anthu olima ku sikumuyi koma sakufuna kutero achotsedwe mu ndondomeko ya mtukula pakhomo komanso maanja omwe akulandira chimanga chaulere. Ife sitili pano kupereka thandizo kwa anthu a manja lende. Kodi mudzalandira zaulere mpaka liti? Anzanu a ma sikimu a Chimwalambango ndi Mkuluwamitete akudzidalira okha ndipo anasiya kulandira zaulere chifukwa akugwiritsa bwino ntchito masikimu awo,” adatero a Kalemba.
Ndipo poyankhapo anthu a m’derali anati madzi omwe amatuluka ku sikimuyi ndi a mchere zomwe akuluakulu a zaulimi m’bomali anati sizomveka chifukwa ngakhale mvula ikugwa, anthu ambiri m’derali sanalowebe mminda mwawo ndi makasu.
Pambali posagwiritsa ntchito sikumuyi, anthu ena odana ndi chitukuko anaba zipangizo zina zomwe a Kalemba alangiza akuluakulu kuti aonetsetse kuti aliyense yemwe anatenga gawo pakubaku aimbidwe mlandu kuti ena aupandu atengerepo phunziro.