Mulipira K1 miliyoni mukathawa kulipira pa “tollgate” -yaopseza RFA

Advertisement

Bungwe la Roads Fund Administration (RFA) lawopseza kuti oyendetsa galimoto omwe agwidwe akudutsa mokakamiza pa ma “tollgate” osalipira ndalama, alipira chindapusa cha ndalama yokwana 1 miliyoni kwacha.

Izi ndi malingana ndi chikalata chomwe bungwe la RFA latulutsa Lachisanu chomwe chikuchenjeza onse oyendetsa galimoto za mtundu uli onse kuti asayesere dara kudutsa pa ma “tollgate” a Chingeni komaso Kalinyeke asanapereke ndalama yomwe akuyenera kupereka.

Bungweli lati chinjezoli ndi kamba koti mchitidwe odutsa mokakamiza, kuthawa kulipira msonkho mu zipata ziwiri zimenezi wachuluka kwambiri ndipo lakumbutsa anthu mdziko muno kuti kuchita choncho ndi mlandu omwe ngati angagwidwe adzalipitsidwa chindapusa.

“Bungwe la Roads Fund Administration (RFA) likuzindikira kuchulukira kwa anthu oyendetsa galimoto omwe akumadutsa mokakamiza pa tollgate osalipira ndalama zomwe amayenera. Bungwe la RFA likufuna kuchenjeza oyendetsa galimoto onse kuti uwu ndi mlandu wotsatira lamulo la 15(1)(a) la RFA (Tolls) Regulations 2021.

“Munthu aliyense amene walephera kutsata lamulo lomwe lili pamwambali ndi wolakwa ndipo akuyenera kulipitsidwa chindapusa cha MK1 miliyoni ndi kukakhala kundende miyezi khumi ndi iwiri,” yatero RFA mu kalatayo.

Bungweli latiso zikachitika kuti munthuyo wayambitsa kuwonongeka kwa njira zolipirirazi, wolakwayo adzayenera alipire ndalama zomwe zidawonongeka komanso ndalama zokonzetsera zinthu zomwe ziwonongekazo.

Advertisement