Mutale Mwanza wapulumuka pa ngozi ya pamsewu

Advertisement

Mutale Mwanza yemwe ndi wachikondi wa oyimba odziwika bwino m’dziko lino, Tay Grin, wapulumuka pa ngozi yomwe inachitika dzulo pa 20 December ku Zambia.

Nkhani yonse ikuti munthawi yomwe ngoziyi imachitika, a Mutale Mwanza amayendera pa galimoto ya mtundu wa Toyota Fortuner yomwe inawombana ndi galimoto ya mtundu wa Toyota Hilux yomwe inali pa tsogolo pawo.

“Dzulo ndinapulumuka pangozi yoopsa yapamsewu Sindikudziwabe kuti izi zinachitika bwanji kunena zoona. Ndinakali okhudzidwa ndipo miyendo yanga sinakhazikike pang’ono koma ndikuthokoza Mulungu chifukwa cha mphatso ya moyo. Ndinali ndekha pamene izi zinkachitika. Pafupifupi sindinakafika 2024. Ndiyamika Mulungu pondisunga moyo wanga. Pempherani NTHAWI ZONSE.” Watelo Mwanza pa tsamba lake la mchezo la Fesibuku.

Pakadali pano Taygrin walonjeza mkazi wakeyu kuti asadandaule zagalimoto pakuti agulirapo ina.

Advertisement