Kuli ng’amba chaka chino, samalani chakudya mu nyengo ya khilisimasi, latero boma


Malawi is expected to experience drought in the 2023/24 farming season

Boma kudzera mu unduna wa zamalimidwe lalangiza anthu kuti asamale chakudya chomwe ali nacho chifukwa ulosi ukusonyeza kuti kuli nga’mba mu chaka cha ulimi cha 2023/24 zomwe zingathe kupangitsa kuchepa kwa chakudya pakhomo.

Mlembi mu Unduna wa malimidwe a Dickxie V. Kampani ndi omwe anena izi potsatira ulosi wa nyengo omwe watulutsidwa ndi nthambi yoona za nyengo ndi kusintha kwa nyengo. Ulosiwu ukuonetsa kuti nyengo ya dzinja ya 2023/2024 ikuyembekezereka kukhudzidwa ndi mphepo ya El Niño imene imapangitsa ng’amba ya nthawi yayitali komanso kusefukira kwa madzi.

A Kampani ati ndikoyenera kuti maanja asamale chakudya chomwe ali nacho makamaka mu nthawi ya zisangalalo monga khilisimasi, chaka chatsopano, ukwati ndi zochitika zina za chikhalidwe.

“Pewani kuononga chakudya pophika chakudya chimene mungakwanitse kudya molingana ndi kukula kwa banja lanu komanso kuchuluka kwa anthu pazochitika zosiyanasiyana

“Panthawi  yomwe chakudya chikupezeka chambiri, onetsetsani kuti mwasunga mitundu yosiyanasiyana potengera kukula kwa banja lanu.  Zakudya zina ziyenera kukonzedwa zisanasungidwe monga kufutsa. Zakudya zomwe zingathe kusungidwa ndi monga masamba, chinangwa, chimanga, nyama, nsomba, za mgulu la nyemba komanso zakudya zimene zimapezeka kwa nthawi yochepa pa chaka,” atero a Kampani.

Iwo atinso anthu awonetsetse kuti asunga chakudya chokwanira banja lonse pa chaka asanagulitse chotsala.

Malingana ndi a zanyengo, maboma ambiri a m’zigawo za kum’mwera ndi pakati alandira mvula yapakatikati komanso yocheperako.

M’madera ena nyengo ya dzinja ikuyembekezereka kuyamba mochedwa ndi masabata awiri ndipo izi zipangitsa kuti mvula yobzalira mbewu ichedwe m’dziko muno.

Kuyambira mwezi wa January kufikira March, madera ambiri ayembekezere mvula yapakatikati komanso yocheperako ndipo ayembekezerenso kulandira mvula yochuluka m’mwezi wa January. Palinso chiopsezo chachikulu cha ng’amba m’mwezi wa February ndipo izi zikhudza kwambiri ntchito zaulimi.

Ulosi wa nyengo ya dzinja ya 2023/2024 wa m’maboma ambiri m’zigawo za kum’mwera ndi pakati ukuonetsa kuti pakhala vuto la kusowa kwa madzi ndipo izi zingathe kupangitsa kuti mbewu zisakule bwino.

Ngakhale pali chiyembekezo cholandira mvula yochulukirapo m’mwezi wa January, kagwedwe ka mvula m’mwezi wa February kadzakhala kosinthasintha komanso kosadalirika.

Unduna wa malimidwe wauza alimi kuti atatile kabzalidwe ka mbewu koyenera kuti akhale ndi chiwerengero cha mbewu choyenera komanso mbewu ikangomera, apakize pomwe siinamere kuti akhale ndi chiwerengero choyenera cha mbewu m’munda

Pomwe mbewu yafota, alimi auzidwaa kuti abzale ina kapena mitundu ina ya mbewu zomwe zimapilira ku ng’amba komanso zocha msanga ndipo athire feteleza okulitsa panthawi yomwe akubzala kapena pakadutsa masiku 7 kuchokera tsiku lomwe abzala kuti mbewu zikule bwino

Alimi awauzanso kuti abzale mitundu ya mbewu yopilira ku ng’amba, kapena mitundu ya chimanga imene imacha msanga.

“Mitundu ya mbewu ndi kabzalidwe koyenera Kubzala mbewu yogwirizana ndi nyengo kumathandiza kuti alimi akolole zochuluka,” undunawu watero

Alimi alangizidwanso kuti abzale chimanga mosakaniza ndi mbewu za m’gulu la nyemba zomwe zimaonjezera chonde m’nthaka monga khobwe, nyemba ndi nandolo komanso abzale mbewu zopilira ku ng’amba monga chinangwa, mawere, mbatata, mapira, thonje, sesame ndi mpendazuwa

Alimi akuyeneranso kuonetsetsa kuti madzi akulowa m’nthaka kuti chinyontho chikhale chokwanira. Izi zimachepetsa mavuto a ng’amba yomwe imatha kubwera mkatikati mwa nyengo ya dzinja.

Atha kuchita izi pomanga zinthu zosiyanasiyana zothandizira kukolola madzi monga matchinga, akalozera, maswale, ngonyeka komanso maenje obzalamo mbewu

Alimi athanso kuthira manyowa okwanira kuti asunge chinyontho komanso kuonjezera chonde m’thaka.