Siyani kuchita nawo ziwonetsero, zilibe phindu – a Malawi alangizidwa

Advertisement

Ngakhale kutenga nawo gawo pa ziwonetsero zili zonse uli ufulu wachibadwidwe, gulu lina lomwe likudzitchula kuti ‘Abwenzi a Atupele Muluzi’, lalangiza anthu m’dziko muno kuti asiye kutenga nawo gawo ponena kuti sizikubweretsa phindu ku dziko lino kamba koti otsogolerawo akumapanga pongofuna kukhutitsa mimba zawo.

Akuluakulu agululi amayankhula izi lachinayi munzinda wa Blantyre pomwe anachititsa nsonkhano wa atolankhani komwe amaikirapo ndemanga pa zinthu zosiyanasiyana zomwe akuti ndizokhudza miyoyo ya anthu m’dziko la Malawi muno.

Malingana ndi mlembi wa nkulu wa gululi la ‘Abwenzi a Atupele Muluzi’ lomwe pachizungu likutchedwa ‘Friends of Atupele Muluzi’ a Stain Chidothe, ndizokhumudwitsa kwambiri kuti ziwonetsero m’dziko muno zinasiya kalekale kubereka zipatso ndipo ati gwelo la zonsezi ndi kamba koti anthu andale ena akhala akulowelera pa ziwonetsero zomwe zakhala zikuchitika m’madera osiyanasiyana m’dziko muno.

A Chidothe anapitilira ndikufotokoza kuti chifukwa china chomwe ziwonetsero sizikubala zipatso ngati kale m’dziko muno, ndi kamba koti anthu ambiri omwe akumatsogolera ziwonetsero pano analowedwa mtima wadyera ndipo anena kuti ambiri mwaiwo akumafuna kupezapo dipo pa ntchito yotsogolera kuchita ziwonetsero, zomwe akuti ndikulakwitsa kwakukulu.

Apa nkuluyu mosafuna kupsatira mawu anapeleka chitsanzo cha ziwonetsero zomwe zinkafuna kuchitika ku Mzuzu miyezi ya m’mbuyomu zomwe akuti zinalepheleka kamba koti nduna zina za boma zinafumbatitsa ndalama kwa akuluakulu omwe ankatsogolera zionetselozi kuphatikizapo a Bon Kalindo.

“Anthu amene akuyambitsa ziwonetsero aja sakumenya nkhondo yofuna kuthandiza a Malawi, mwa chitsanzo Bon Kalindo anayankhula yekha kuti a Malawi siowafera pamene iye yemwe wakhala akunena kuti amachititsa ziwonetsero pofuna kuwathandiza a Malawi. Anthu ngati awa akumati akalandira ndalama akumakhala pansi ndipo zikatha ndalamazo akumauzaso anthu kuti apite ku ziwonetsero zina.

“Ziwonetsero zose zomwe anapanga palibe chomwe anayankhidwapo ndi boma zomwe zikuonetseratu kuti tsogolo palibe ndipo ndizongofuna kupatsa mkwiyo a Malawi. Ine umboni ndili nawo okwanira bwino, paja ndinali membala wa CCTV ndiye zinthuzi ndikuzidziwa bwino nchifukwa chake ndi kuti a Malawi siyani kutenga nawo gawo pa ziwonetsero, anthuwa akungofuna kutidyera masuku pa mutu basi,” watelo Chidothe.

Podziwa kuti kutsutsa galu mkukumba, nkuluyu anapitilira ndikufotokoza kuti anawona ndi maso ake akuluakulu ena a boma aku akupeleka ndalama kwa anthu omwe ankatsogolera ziwonetselo zomwe zinkafuna kuchitika ku Mzuzu ndicholinga choti ziwonetserozo zilepheleke ndipo akuti zinalephelekedi.

“Gulu lathu motsogozedwa ndi a Kalindo tinachititsa ziwonetsero ku Blantyre komaso Zomba ndipo pomwe ziwonetserozi zinkayenera kuchitikaso ku Mzuzu, nduna zina za boma zinatiyitana. Aliyese otsogolera anapatsidwa K500,000 kuti ziwonetserozi zisachitike. Ine ndekha ndinakana kulandira ndalama imeneyi. Nde mutha kuwona kuti ziwonetsero pano sizimaphula kanthu,” anawonjezera Chidothe.

Iwo ati kuwopsa kwa zonsezi ndi koti pali kuthekera koti anthu m’dziko muno atha kukhala ndi nkwiyo wochuluka ndipo zotsatira zake adzavota mowawidwa mtima zomwe akuti zitha kupangitsa kuti anthu omwe alibe mphatso ya utsogoleri avoteledwe, pambuyo pake kupitilira kuika dziko lino pa mavuto adzaoneni.

Apa a Chidothe alimbikitsa anthu m’dziko muno kuti adzavotele Atupele Muluzi ponena kuti ndi munthu yekhayo yemwe ali ndi kuthekera kotukura m’dziko lino ndipo wanenetsa kuti ino sinthawi yoti anthu adzivotera munthu kamba ka chipani koma wati anthu adzavotele munthu yemwe mfundo zake ndizopeleka chiyembekezo kwa a Malawi.

Advertisement