Banki ya dziko lonse yayambanso kuthandiza Malawi

Advertisement
President Lazarus Chakwera during the launch of the Katunga -Maseya (KAMA) cooperative Mega Farm in Chikwawa district in October 2023

Kwa nthawi yoyamba tsopano kuchokera mchaka cha 2017, banki yayikulu pa dziko lonse ya World Bank yalengeza kuti ipeleka thandizo loti lithandizile mundondomeko yazachuma mdziko lino.

Ndipo padakali pano yapereka ndalama zokwana 137 miliyoni dollars zomwe ndi pafupifupi 230 billion kwacha zithandizira ntchito zachuma ndi zina.

Izi zadza kudzera mchikalata chomwe bankiyi yatulutsa, iyo yati ndiyokhutira kamba kakuti dziko lino lakwanilitsa zina mwa ndondomeko za bungwe la IMF kudzera mu extended credit facility.

Bankiyi yatinso iyo ndiyokhutira malingana ndi momwe dziko la Malawi pansi pa ulanuliro wa a Lazarus Chakwera layendetsera mfundo zake za ndondomeko zokhudza zachuma.

Iyo yatinso ndiyosangalala kamba ka ndondomeko zomwe dziko lino lidakhazikitsa pofuna kuti chuma cha dziko lino chibwelere m’chimake.

Wolemba: Ben Bongololo

Advertisement