Kulinji ku DPP lero? Nsonkhano wa NGC

Advertisement
Bright Msaka, Jappie Mhango and other DPP members

Dzulo lachiwiri tinasiyira poti khothi ku Lilongwe lakana kupeleka chiletso kwa Grezelder Jeffrey chomwe mwa zina chimafuna kuletsa mbali ya mtsogoleri wa chipanichi a Peter Mutharika kuchititsa msonkhano wa akuluakulu a chipani (NGC), ndipo titha kutsimikiza kuti msonkhanowu ulipo ku Mangochi lero, tiyeni tiyembekeze zambiri.

 Akuluakulu a chipani cholamula chakalechi lero akhamukira ku hotela ya Sunbird Nkopola m’boma la Mangochi komwe kukuchitika mkumano wa akuluakulu, ndipo pali chiyembekezo choti mkumanowu ukhazikitsa ma siku omwe chipanichi chichititse nsonkhano waukulu, komveshoni.

Malingana ndi zithunzi zomwe zikuzungulira m’masamba anchezo, ena mwa akuluakulu omwe afika kale kumkumanowu ndi monga a Ken Nsonda, Chimwemwe Chipungu, Jappie Mhango, kungotchulapo ochepa chabe ndipo a Mutharika ndi omwe akuyembekezeka kutsogolera zonse ku msonkhanowo.

Izi zikubwera pomwe bwalo la milandu lapeleka chiletso ku mbali ya a Mutharika choletsa kukwanilitsidwa kwa mfundo zomwe zinakambidwa pa nkumano wa NGC omwe anaitanitsa a Jeffrey masiku apitawo munzinda wa Lilongwe.

Mbali ya a Jeffrey inakambirana kuti komveshoni ya chipanichi ichitika kuyambira lachisanu pa 15 December mpaka loweruka pa 16 December, 2023 munzinda wa Lilongwe koma potsatira chiletsochi, komveshoniyi sichitikaso monga momwe anakozera.

Zitatele, a Mutharika anachotsa a Jeffrey paudindo wa mlembi wamkulu ndipo anawasankha kukhala wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipanichi mchigawo chapakati zomwe sizinawasangalatse a Jeffrey ndipo anapita ku khothi kukatenga chiletso koma pempho lawo lawomba. Mgolo.

Bata likukanika kubwelera mchipani cha Democratic Progressive ndipo zikuoneka kuti maudindo ndiwo gwero lalikuru la kukokana kokana.

Advertisement