Anthu am’mudzi mwa Chimombo awona ngati kutulo atapha njoka 301 lero

Advertisement
Malawi Dedza

Zina ukamva kamba anga mwala, zina zikamachitika nkumati kodi  ndiku Malawi komkuno? Inu anthu am’mudzi mwa Chimombo mdera la mfumu yayikulu Kachere m’boma la Dedza lero pa 12 December ali kukamwa yasa atapha njoka 301 m’munda wina.

Nkhani yonse ikuti anthu ena anawona njoka ziwili zikulowa pa dzenje m’mundawo kenako iwo anaganiza zoti akumbe kuti aphe njokazo. Apa ndipamene anapezana ndi chimkwang’wang’wa cha njokazo. Malipoti akuti anapeza mazira omwe amati akaphwanya mumatuluka njoka.

Anthu am’mudzimo sanagonje koma kupha njoka zonse 301 monga momwe mukuonera pa chithunzipo.

Inu zina ukamva ngati malodza ndipo anthu ammudzimo ali kakasi pakuti malodza amtundu onga iwu aka mkoyamba kuchitika m’mudzimo.

Wolemba: Ben Bongololo

Advertisement