A Maxwell James a zaka 23 zakubadwa akusungidwa mchitokosi cha apolisi ku Phalombe kamba kopezeka ndi ndalama zachinyengo zokwana K240,000.
Nkhani yonse ikuti pa 9 December a James adapita ku msika wawukulu wa Mulomba komwe iwo ankafuna kuyika ndalamazo mu lamya kudzera kwa ejenti wa Mpamba komanso Aitel Money.
Ejent atayika ndalama zokwana K155,000 mu lamya yamkuluyo adadabwa atalandira ndalama zachinyengo. Apa Enjentiyo sanachitire mwina koma kukoka chingwe ku polisi ya Mulomba kuwadziwitsa za Nkhaniyi.
Apa apolisi sanazengereze kuthamangira pa malowo ndipo atafika adapeza a James ali ndi ma K5,000 ankhaninkhani okwana K240,000 koma chodabwitsa mchakuti ndalamazi zonse zinali za nambala ya chinsinsi yofanana kuphelezera kuti katakweyi adali kusungadi ndalama ya chinyengo.
Pakadali pano yemwe ndi mneneri wa apolisi m’bomali a Jimmy Kapanja atsimikiza zankhaniyi ndipo a James akuyembekezereka kukaonekera ku bwalo la milandu kukayankha mlandu opezeka ndi khobidi la chinyengo.
A Maxwell James amachokera m’mudzi wa Manjawira mfumu yayikulu Phambala m’boma la Ntcheu.
Wolemba: Ben Bongololo