Yapamphanthidwa ngati wakuba foni

Advertisement

Kunali mkoke mkoke lero mu Tnm Super League pamene anyamata amakudzulana nthenga, kugwalulana zibwano, kuchotsana chimbenene. Uyu ndi tsatanetsane wamomwe lero masewero athera.

Mighty Wanderers yalepherana ndi timu ya Bangwe All Stars, ndipo masewero athera 0 kwa 0.

Asilikali a Kamuzu Barracks akuntha ndikufinya kholingo anyamata a Civo Service United ndi Zigoli ziwiri kwa chimodzi.

Fomo yachapa anyamata a Chitipa United ndi Chigoli chimodzi ndi kwa sitikupanga nawo kapena kuti abwelera chimanjamanja.

Karonga United yatsukuluza anyamata a Mighty Tigers ndi zigoli zitatu kwa chimodzi. Ingwina zanu Karonga zaboola akambuku amenewa ndi zigoli zitatu kwa chimodzi. Kufafantha komanso kukhaulitsa motheratu.

Moyale Barracks ndi anyamata a Dedza Dynamos masewero athera 0-0 munzinda wa Mzuzu.

Umu ndi momwe masewero athera lero pa 28 April, dzakhaleni pompa sabata la mawa pamene matibu adzakhale akupitilira kuchotsana chimbenene mu Tnm Super League 

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.