Khilisimisi ivutilapo chaka chino, fanta wakwera mtengo

Advertisement

Anthu omwe akuyembekeza kukhala ndi miyambo ngati ukwati ndi ina yomwe zakumwa zozizilitsa kukhosi zimafunika, alimbe mthumba chifukwa fanta, Coca-cola ndi azinzake akwera mtengo, ndipo nkhawa yagwira ana kuti mwina chaka chino khilisimisi itha kulepheleka chifukwa nde kwawilira.

Kampani ya Coca-Cola Beverages Malawi yomwe imapanga zakumwa zozizilitsa kukhosi  yalengeza kuti yakweza mitengo yazakumwa zake zonse.

Malingana ndi chikalata chomwe kampaniyi yatulutsa lachitatu chomwe chasainidwa ndi m’modzi mwa akuluakulu awo a Josephine Msalilwa, mitengoyi yakwezedwa potsatira kugwa mphamvu kwa ndalama ya Kwacha sabata yatha.

Chikalatachi chati kuyambira pano botolo la ma lita awiri (2 liters) la Sobo Squash lakwezedwa kuchoka pa K3,700 kufika pa K6000, Coca-cola (300 ml RGB) wachoka pa K450 kufika pa K650, botolo la madzi K550 kuchoka pa K350, sobo (300ml), adzigulitsidwa pa K600 kuchoka pa K400.

Mbali inayi, botolo a Coca-cola (300ml PET) lakwezedwa kufika pa K800 kuchoka pa K500 pamene botolo la Sobo (300 ml PET) lakwezedwa kuchoka pa K500 kufika pa K700.

Izi zikutanthauza kuti onse omwe akukoza miyambo yomwe zakumwazi zikuyenera kukamwedwa kuphatikizapo maukwati ndi zisangalaro zina, akuyenera kupisaso m’matumba mwawo ndikuwonjezera pa ma bajeti omwe anakoza.

Kupatula apo, makolo akuyenera kukozekera bwino kuti ana wawo adzasangalare atanyamula ma botolo azakumwazi pa zisangalaro za khilisimisi komaso chaka chatsopano monga momwe zimachitikira dzaka dzonse.

Pomwe banki yaikulu sabata yatha inalengeza kuti ndalama ya kwacha yachepa mphamvu, makampani ochuluka akupitilira kukweza mitengo ya zinthu zomwe a map anga.

Advertisement