Mukaona mbendera petupetu, magetsi waliwali komaso apolisi atayima m’misewu, dziwani tate wa dziko lino wafika kuchokera kunja; a Lazarus Chakwera akubwera lero komatu apeza zinthu zambiri zakwera mtengo. Kapena a Chakwera abwera ndi mayankho?
A Chakwera ananyamuka m’dziko muno Lachitatu kupita m’dziko la Saudi Arabia komwe amkayenera kukakhala nawo pa mkumano wa pakati pa mayiko a mu Africa komaso maiko a luya omwe umatchedwa ‘Africa-Arab Summit’ koma unalepheleka patatsala ma ola ochepa.
M’malo mwache, mtsogoleri wa dzikoyu anachita zokambirana ndi akuluakulu a zamalonda m’dziko la Saudi Arabia kuphatikizapo bungwe la Saudi Development Fund lomwe linapeleka ku dziko lino ndalama za nkhani nkhani zokozera nsewu wa Mangochi-Makanjira.
Atamaliza zochitika zake m’dziko la Saudi Arabia, a Chakwera anakakhala nawo pa chiwonetsero chachitatu cha zamalonda chomwe chimatchedwa Intra-African Trade Fair (IATF2023) chomwe chinachitikira ku Cairo m’dziko la Egypt pa 13 November, 2023.
Uku mtsogoleriyu wati wasainirana mgwirizano ndi bank ya Afrexim yomwe akuti yapeleka ku dziko lino ndalama zokwa 2 biliyoni za m’dziko la America zomwe ndizopitilira 3 thililiyoni kwacha (K3 trillion) zomwe zithandize ntchito za chitukuko.
Pakadali pano malipoti akusonyeza kuti a Chakwera anyamuka kale m’dziko la Egypt kubwlera kuno ku mudzi ndipo afika kudzera pa bwalo la ndege la Kamuzu International munzinda wa Lilongwe.
Malingana ndimomwe ananenera akuluakulu a boma pomwe a Chakwera amanyamuka mdziko mumo, ndege yomwe yanyamula mtsogoleri wa dzikoyu komaso anthu ena omwe anatsagana nawo paulendowu, ikuyembekezeka kufika pa bwalo la Kamuzu International nthawi ikamati 13:35 masana ano.
Zonsezi zikuchitika pomwe mitengo ya katundu osiyanasiyana yakwera kutsatira kugwa mphamvu kwa ndalama ya dziko lino lachiwiri sabata latha zinthu.