Chakwera wakuwizidwa

Advertisement
Convoy for President of Malawi Lazarus Chakwera

Anthu m’boma la Lilongwe anaiwala kuti mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera anali pa chisoni pomwe anamukuwiza kuti “tipatse mafuta” nthawi yomwe amachokera ku mwambo oyika m’manda malemu John Tembo.

Lachitatu pa 4 October, 2023, a Chakwera anali m’mudzi mwa Kaphala mfumu yaikulu Kaphuka m’boma la Dedza komwe thupi la mtsogoleri wakale wa chipani cha Malawi Congress (MCP), a Tembo limayikidwa m’manda.

Pomwe mtsogoleri wa dziko linoyu amachokera ku mwambo wa chisoniwu, anthu ena omwe anayalana mphepete mwa nsewu wina anayamba kumukuwiza.

Malingana ndi kanema yomwe anthu akugawana m’masamba a nchezo, anthuwa mwa zina amamuuza tate wa dzikoyu kuti awapatse mafuta a galimoto omwe pano akusowa ngati nzungu wa misala.

Mkatikati mwa mfuu komaso malikhwelu, anthu enaso akuveka mu kanemayi akumuuza Chakwera kuti amutopera, pamene ena akufusana kuti mdipiti wa mtsogoleri wadzikowo wagwiritsa ntchito mafuta ochuluka bwanji?

“Iwe! Iwe! Iwe! Mafuta tilibe ife. Tipatse mafuta iwe. Tikufuna mafuta ife.

“Magalimoto onsewa palowa mafuta ndi ndalama zingati pamenepa,” anafusana anthu okwiyawo.

Izi zikudza pomwe kusowa kwa mafuta a galimoto kwafika posauzana m’madera ambiri m’dziko muno.

Advertisement