Ati Jetu akuzunzidwa – atero a Podcast Malawi

Advertisement
Musician Jetu from Malawi

Ati n’kutheka kuti kukondwa kwanu ndi nyimbo ya Chakwaza kukubwera chabe chifukwa mumakonda kuzunza nkhalamba, atero amuna a pa Podcast Malawi.

Mkozi wa nyimbo Dumisani Moyo yemwe amatchuka kwambiri ndi dzina loti Blage, ndi m’modzi mwa anthu omwe akuona kuti mwa Jetu mulibe tsogolo pa nkhani ya mayimbidwe ngakhale kuti pano gogoyu watekesa pa Malawi ndi nyimbo yake yatsopano ya ‘Chakwaza’.

Blage wayankhula maganizo akewa mu kanema yemwe watulutsidwa Lachinayi ndi Podcast Malawi mu pologalamu ya ‘Hit O Miss’ yomwe akatswiri pa mayimbidwe amakhala akuzukuta mozama momwe lunso la mayimbidwe likuyendera m’dziko muno.

Mukanemayu, Blage wanenetsa kuti Jetu siwoyimba ndipo wati m’dziko muno ngati muli nzira zembe pa mayimbidwe yemwe akuyenera kuvulilidwa chisoti, ndi a Gidess Chalamanda okha basi.

“Nyimboyi imayenera kukhala ya munthu amene amabakira uja chifukwa ndi mbali yokhayo yomwe ikumavekako, komano pa iyeyo Jetu-yo, ndisaname aaaa. Anthu opanga nyimbo timawatchula kuti artist kutanthauza kuti pamakhala luso lina lake, koma palibe luso lili lonse pa Jetu. Ngati tikunena za anthu akuluakulu, tiyeni tidziwapopa a Gidess,” watelo Blage.

Kupatula apo, Blage analembaso pa tsamba lake la fesibuku kunena kuti ngati pali chinthu chomwe gogo Jetu akuyenera kuchita kuti naye asangalare ndikusiya kuyimba basi.

Mukanema wa Podcast Malawi yemweyu, naye Brendon Jones anagwirizana ndi Blage ponena kuti nyimbo ya  ya ‘Chakwaza’ imayenera kukhala ya amene anabakila koma wati nkutheka kuti amaopa kuti akakhala patsogolo munthu ameneyo nyimboyo siyingatchuke ngati momwe yachitira.

Brendon anati poyamba anali osangalatsidwa kuti gogo Jetu anayamba kuyimba koma wati anakhumudwa atazindikira kuti akamajambula nyimbo zake, gogoyu yemwe ali ndi zaka 72, amakalipilidwa ngati mwana.

“Ineyo ndinali osangalatsidwa ndi idea yoti Jetu aziyimba koma kuti ndiyambe kudana nawo, ndinawonera momwe zimakhalira akamajambula nyimbo (behind the scene). Agogo aja amakalipidwa, amawashisha kwambiri, pena kukanika kuyenda zomwe sizinandisangalatse,” anatelo Brendon. 

Nkuluyu wati kukalipilidwa kwa Jetu ndi anyamata ake ndichitsimikizo choti gogoyu akuchita kukakamizidwa kuchita zinthu zomwe simbali yake ndipo wati munthu wa luso lenileni loyimba sumachita kumukakamiza kapena kumuuza zochita.

“Mwachitsazo a Gidess amangoimba ndipo ngakhale lero a Gidess atha kulemba nyimbo ndikuimbaso bwino osaphonya. A Jetu anapita ku show inayake mpaka microphone ankawatembenuza zomwe zinali zochititsa manyazi. Kwa ineyo ndimaona kuti nzokakamizidwa. Inde nyimbo zawo zikufala koma maganizo oyimbawo si awo akungogwiritsidwa ntchito basi,” wateloso Brendon.

Zomwe makosanawa ayankhula zadzetsa mtsutso waukulu kamba koti anthu ena omwe akusangalatsidwa ndi Jetu akuti uku sikuyankhula kwabwino.

“Dumisani Blage Moyo please tisiyileni jetu wathu ngati sakusangalasani zanu osamapanga ma podcast kumanyoza athu muzitolere azibambo,” watelo Eva Makaka poyikira ndemanga pa tsamba lina la fesibuku za nkhaniyi.

Ngakhale zili choncho, anthu ena akuikira kumbuyo zomwe anthuwa ayankhula ponena kuti Jetu akudyeledwadi masuku pamutu ndi anthu omwe amamutsogolera pa mayimbidwe ake.

“Paja chilungamo chimawawa eti? Moti inuyo simukuona kuti Jetu akuchita kukakamizidwa? Munthuyu siwoyimba ndipo sindikuona vuto pa zomwe wayankhula Blage. Vuto a Malawi timasangalala munthu akamatinamiza, big up man Blage,” Wateloso Yotamu Kashoti poikira ndemanga za nkhaniyi pa fesibuku.

Jetu yemwe dzina lake lenileni ndi Christina Malaya, anabadwa chaka cha 1952 ndipo pano akukhala ku Bangwe mu mzinda wa Blantyre.

Advertisement

One Comment

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.