Kwabhebha ndi ku Illusionz kukubwera Dj Maphorisa; mitengo yafika mpaka K850,000

Advertisement
DJ Maphorisa appears on a poster for Illusionz club launch

Inde oyimba Wikise anati K10 sauzande sungamange nyumba, komatu K850 sauzande ndiyambiri zedi: a Malawi mukuitanidwa kukaipatsa moto, kukapinda ziwuno, kudikura ndi Dj Mapholisa, komatu mulimbe mthumba, kuli vimitengo anga ukugula puloti.

Lachisanu pa 20 October chaka chino, kuli kutsekulira malo ochitira zisangalaro a Illusionz omwe akupezekera ku Golden Peacock Complex mumzinda wa Lilongwe.

Ngati njira imodzi yobweretsa chikoka kuti anthu mazana mazana azapezeke nawo ku mwambo otsekulira malo azachisangalarowa, omwe akuyendetsa zokozekera mwambowu anaganiza zodzakhala ndi phwando la mayimbidwe ndi mavinidwe.

Mwaichi, akuluakulu oyendetsa mwambowu ayitana oyimba wa m’dziko la South Africa Themba Sekowe yemwe amadziwika bwino ndi dzina loti Dj Maphorisa kuti asangalatse anthu.

Komatu mitengo yomwe yakhazikitsidwa kuti anthu akalipire yadolora a Malawi omwe ena kudzera m’masamba anchezo akuti ichi ndi chibwana cha nchombo lende.

Mwa chitsanzo, munthu wamba amene saguliratu tikiti lisanafike tsikuli, akuyenera kudzapeleka ma K5000 okwana 6 (K30,000) kuti naye alowe ndikuipatsa moto uku akuchita chakumwa chaukali.

Komatu mtengo omwe wadzetsa manong’onong’o siumenewo, kuli mitengo ya anthu ofunika (VIP) omwe a kuti azikakhala m’matebulo.

Tebulo yotchipilako ndi ya anthu asanu ndi m’modzi (6), iwowa akuyenera kukalipira K400 sausande ndipo yotsatana nayo ndi ya anthu asanu ndi atatu (8) omwe akuyenera kukalipira K550 sauzande.

Kupatula apo, kuliso mitengo monga K600 sauzande, K750 sauzande, K800 sauzande ndipo mtengo odulitsitsa ndi K850 sauzande pa tebulo ya anthu khumi (10) ndipo gulu ili ndi lomwe likuyembekezeka kukanjoya kuposa ena onse.

Mwa zina anthu omwe akakhale m’magulu a makhumutchawa azikapatsidwa nyama komaso mitundu ya mowa osiyanasiyana motengera ndi mtengo wa matebulo omwe akakhale.

Advertisement