Moto wa Jetu ukana kuzilala, apata puloti

Advertisement

Chinantindi cha anthu chikupitiriza kutsata ndi kukonda Jetu ngakhale kuti makosana a Podcast Malawi anapereka ganizo lakuti gogoyu asiye kuyimba chifukwa alibe luso pamayimbidwe.

Patangopita masiku ochepa chabe a Podcast Malawi chiyakhulireni zokhwatcha Jetu, gogoyu wakatekesa ku sukulu yaukachenjede ya MUBAS mzinda wa Blantyre.

Ophunzira pa sukuluyi sanawerengere nkomwe zomwe Podcast Malawi inayankhula ndipo anamunyadira gogoyu mwamsangala pomwe amayimba.

Mopatsa chidwi, mumasiku ochepa omwewa Jetu waninkhidwa puloti yoti amangepo nyumba. Ulemu ukupita kwa Dorothy, mkazi wake wa woyimba Zeze Kingston,  pomema anthu omwe amamutsata pa tsamba lake la fesibuku kuti asonkhe limodzi limodzi kuti akamugulire Jetu puloti yoti amangepo nyumba.

“Pa page pa tilipo anthu more  than 400 thousand. Aliyense kuponya K1000 for Jetu it means we can raise K400,000,000 eti, then she can buy the plot, build a house and go to John eti. Munthu asamakome akafa. koma we need a neutral person for accountability and for the money to be used for its course. Adzukulu atha kulowetsa zibwana,” analemba choncho mayi Kingston.

Ngati chitsimikizo choti gogoyu akukondedwadi ndi khwimbi la anthu, patangopita ma ola ochepa chabe, Dorothy analembanso pa tsamba lakeli kuwulura kuti kampani yogulitsa malo ya Eagles Real Estate Consultants, yadzipeleka kuti imusupa Jetu puloti yoti amangepo nyumba.

“Plot ya Jetu yapezeka. Eagles Real Estate Consultants to gift Jetu a plot of Land. Tisakeno yomangila. Inunso mukafuna malo kaguleni anu ku Eagles,” analembaso choncho Dorothy pa tsamba lakelo.

Poyankhula ndi tsamba lino, mayi Kingston ati tsapano ali kalikiliki kukambirana ndi makampani a ma foni kuti awapangire manambala omwe anthu angamatumizileko ndalama zomwe zigwire ntchito pomumangira Jetu nyumba.

Dorothy wati pali chiyembekezo kuti ma nambalawa akhala atapangidwa pomafika Lachinayi sabata ino ndipo wati zonse zikatheka anthu adzadziwitsidwa manambala omwe angamatumizile ndalama yothandizira kumangira nyumba gogoyu.

Mayi Kingston analembanso pa tsamba lawo la fesibuku kuti ganizoli ladza polingalira kuti Jetu anabeleka ana asanu ndi anayi (9), koma 8 anamwalira ndipo m’modzi yemwe anatsalayo pano anatchonaso ku South Africa ndipo samawathandiza mokwanira.

Dorothy wati gogo Jetu pamodzi ndi zidzukulu zisanu (5) zomwe malemu ana awo anazisiya, amakhala nyumba ya chipinda chimodzi ndipo akuti onsewa amathandizidwa ndi mdzukulu wa mkulu, yemweso akuwatsogolera pa mayimbidwe.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.