Timangofuna tikuoneni – Khuda wati banja silinathe

Advertisement
Malawians football player Khuda Myaba

Nyimbo ya ‘Atambwali okhaokha’ ya Gibo Pearson ndi yomwe katswiri wosewera mpira wamiyendo, Khuda Myaba, akumvera pano kamba koti zoti banja lake latha ndi nkazi wake Enlecio, zinali nthabwala chabe ndipo wati iyeyo anakonda hule yemweyo.

Lamulungu, Myaba anadzidzimutsa anthu pomwe analengeza kuti banja lake ndi osewera watimu ya Scorchers, Enlecio Mhango latha ponena kuti mkaziyo akumayendayenda m’malo omwela mowa.

Osewera mpirayu yemwe pano akusewelera mpira wake m’dziko la Syria, analemba patsamba lake la fesibuku kuti nthiti yakeyo yakhala ikumapita kumalo omwera mowa kukapanga zogulitsa thupi zomwe anadandaula nazo ponena kuti iye sanakwatile nkazi oyenda yenda.

“Ndikufuna kuti anthu aziwe chilungamo ineyo ndi Enlecio Monalisa Mhango BANJA latha. Wakhala akutuluka nyumba pomwe ine ndili South Africa komaso kuno ku Syria, amapita ma night club kumapanga uhule ngati ineyo sinditumiza ndalama chosecho amapita ma night club kukawononga ndalama zomwe ndimakhala ndikumutumizila.

“Nde pano mukamamuona Ali ndi amuna ena ziwani kuti banja ndi khuda Myaba linatha ine sinakwatile hule kuti azikhalila ma bar ayi. Pano ndikumufunila kunjoya kwambiri,” watelo Khuda uthenga wake pa fesibuku.

Koma patadutsa maola ochepa Khuda analembaso patsamba lake kuti zomwe amaneneza anali macheza chabe ndipo wati amafuna kuti awone ndikumva zomwe anthu angayankhule pa nkhani za banja lakezo.

Iye wati Enlecio wachoka naye kutali alibe kena kalikose choncho sangamusiye pano ndipo watsindika kuti kaya anthu adzimuseka kuti nkazi wake amapita m’mabara, palibe vuto ponena kuti iye anakonda hul* yemweyo.

“This was expensive prank. (Izi zinali zochita kukonza) Just imagine the news has been in all social media platforms. (tangoganizani nkhani ili m’masamba anchezo ochuluka) You think I will leave my wife even (mukuganiza ndingamusiye nkazi wanga ngakhale) tamupeza akupanga chigololo? She has been there for me ndilibe kalikonse ndiliku moyale pano ndalemba kuti banja latha eti ife timaziwa kazi ndi hule chosecho anthu akupanga zimenezo kukhala azizake a kadzi wanga.

“Ndinu agalu kwambiri Ndipo Kaya muzimuona kuma bar ndiwanga ndinakonda hule yemweyu. I just post about it 2 mins ma message ambiri Azikadzi ku inbox kwanga aaaa amalawi chonde ife ndi kazi uyu tachoka kutali mwamva? Ndinu agalu kwambiri,” watelo Khuda.

Kupatula kulemba pa tsamba lakelo, osewera mpirayu anazijambulaso kanema akufotokoza tsatanetsatane wa nkhaniyi ndipo wanenetsa kuti banja lake silingathe ndi Enlecio ponena kuti awiriwa anayanjana magazi.

Iye wati pakadali pano madongosolo alinkati kuti amugulire nkazi wakeyo njale yoyendera ndipo wanenetsa kuti a Malawi onse omwe amamuchitira dumbo, apeze zina zochita ponena kuti iyeyo ndikuchikweza, sangankwanitse.

Advertisement