Awiri amangidwa chifukwa cholima chamba ku Mzimba

Advertisement

A Polisi ya Jenda m’boma la Mzimba, amanga anthu awiri omwe ndi Julius Zgambo (27) ndi Alfred Zimba (22) kamba kolima chamba popanda Chilolezo ku Vibangalala m’bomalo.

M’neneri wa Polisi ya Jenda, Sub Inspector Macfarlen Mseteka, wauza Malawi24 kuti awiriwa anamangidwa usiku wa pa 5–6 May 2024, a Polisi atasinidwa khutu kuti amalima chamba  m’derali.

A Mseteka awonjezera ponena kuti a Zgambo adalima mitengo ya chamba yokwana 350 ndi china cholemera makilogalamu awiri, pomwe Zimba adapezeka ndi mbewu 100 za chamba m’munda mwake. Awiriwo adalephera kuwonetsa makalata achilolezo.

Iwo akaimbidwa mlandu wolima komanso kupezeka ndi chamba popanda chilolezo, ndipo akaonekera kubwalo lamilandu posachedwapa.

Awiriwa amachokera m’dera la Vibangalala mfumu yayikulu Mzukuzuku m’boma lomwero la Mzimba.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.